Kodi Munayatsapo Nkhalango?
MUKUNENA KUTI, ndithudi ayi. Koma taimani! Mwinamwake munatero. Mvetserani mawu a wophunzira Yakobo akuti: “Lilimenso lili chiŵalo chaching’ono, ndipo lidzikuzira zazikulu. Taonani, kamoto kakang’ono kayatsa nkhuni zambiri!”—Yakobo 3:5.
Lilime ndichiŵalo chofunika cholankhulira, koma ha ndimotani nanga mmene chagwiritsidwira ntchito moipa! Anthu amagwiritsira ntchito lilime kunama ndi kuneneza ena. Amasuliza ena mwankhanza ndi lilime, kuipitsa mbiri yawo, ndi kuwanyenga. Oyambitsa chiwawa amagwiritsira ntchito lilime kusonkhezera chipanduko. Adolf Hitler anagwiritsira ntchito lilime lake kusonkhanitsa anthu kuti achite nkhondo—‘kuyatsadi nkhalango’!
Ngakhale anthu okhala ndi cholinga chabwino ‘angayatse nkhalango’ zazing’ono. Kodi munayamba mwanenapo kanthu ndipo mwamsanga kukhumba kuti simukananena kanthuko? Ngati ndichoncho, mwazindikira zimene Yakobo akutanthauza pamene anati: “Lilime palibe munthu akhoza kulizoloŵeretsa.”—Yakobo 3:8.
Komabe, tingayese kugwiritsira ntchito lilime lathu mwaubwino. Mofanana ndi wamasalmo, tinganene motsimikiza kuti: “Ndidzasunga njira zanga, kuti ndingachimwe ndi lilime langa.” (Salmo 39:1) Mmalo mwakusuliza anthu ena mwankhanza, tingayese kuwamangirira. Mmalo mwakuneneza ena, tingayamikire anthuwo. Mmalo mwakuchita psete ndi kuchita chinyengo, tinganene chowonadi ndi kulangiza. Pamene lisonkhezeredwa ndi mtima wabwino, lilime linganene mawu abwino ochiritsa. Yesu anagwiritsira ntchito lilime lake mwanjira yabwino kwambiri kuphunzitsa anthu za chipulumutso.
Zowonadi, “lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo.” (Miyambo 18:21) Kodi lilime lanu ndilakupha kapena lopulumutsa moyo? Kodi ‘limayatsa nkhalango’ kapena limazimitsa? Wamasalmo anapemphera kwa Mulungu kuti: “Lilime langa liimbire mawu anu; pakuti malamulo anu onse ndiwo olungama.” (Salmo 119:172) Ngati tikulitsa mkhalidwe wamaganizo wa wamasalmo, nafenso tidzagwiritsira ntchito lilime lathu bwino.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Chithunzithunzi cha U.S. Forest Service