Kodi Kuthiridwa Mwazi Kumathokozedwa Mopambanitsa?
Kuthiridwa mwazi nkofala m’mankhwala amakono, koma kodi iko kuli kwabwino mogwirizana ndi kutchuka kwakeko? Kodi mukulingalira motani?
M’magazini akuti The American Journal of Medicine (February 1993), Dr. Craig S. Kitchens anafunsa kuti: “Kodi Kuthiridwa Mwazi Kumathokozedwa Mopambanitsa?” Iye ananena kuti madokotala amapenda mosamalitsa kaya ngati phindu la kuchiritsa kwakutikwakuti nlalikulu kuposa upandu umene kungachititse. Bwanji ponena za kuthiridwa mwazi?
Kitchens anapenda umboni waposachedwapa wa maupandu ambiri ogwirizanitsidwa ndi kuthiridwa mwazi, monga ngati kutupa chiŵindi, kuwonongeka kwa dongosolo lotetezera thupi kumatenda, kulephera kugwira ntchito kwa ziŵalo za m’thupi, ndi matenda ochititsidwa ndi kuikidwa chiŵalo cha munthu wina. Kupenda kwina kumene kunanena mwachidule za “zovuta zikwizikwi” zochititsidwa ndi kuthiridwa mwazi “kunagamula kuti kuthiridwa mwazi kulikonse kuli ndi kuthekera kwa 20% kwa kuchititsa mavuto, ena aang’ono koma ena owopsa,” ngakhale akupha.
Komabe, kodi mapindu olingaliridwawo amalungamitsa kuyang’anizana ndi maupanduwo?
Dr. Kitchens anapenda kufufuza kochitiridwa lipoti kokwanira 16 koloŵetsamo maopaleshoni okwanira 1,404 ochitidwa pa Mboni za Yehova, zimene zimakana kuthiridwa mwazi kaamba komvera lamulo la Baibulo la ‘kusala mwazi.’—Machitidwe 15:28, 29.
Kodi zotulukapo zinali zotani? “Chosankha cha odwala a Mboni za Yehova cha kukana kuthiridwa mwazi pamaopaleshoni aakulu chikuoneka kuti chinawonjezera 0.5% kufikira 1.5% yokha ya kuthekera kwa imfa kuyerekezera ndi upandu wonse wa opaleshoni. Chosadziŵika bwino lomwe ndicho ukulu wa kudwala ndi imfa umene umapeŵedwa mwa maopaleshoni otero, koma mwinamwake ukuluwo umapambana upandu wa kusathiridwa mwazi.” (Kanyenye ngwathu.) Kodi mfundo yake inali yotani? Upandu uliwonse wa mankhwala wa kukana kuthiridwa mwazi mwinamwake uli waung’ono koposa maupandu oloŵetsedwamo m’kuvomereza kuthiridwa mwazi.
Chotero, nchifukwa chake Kitchens anafunsa funso lanzeru lakuti: “Ngati kusathira mwazi Mboni za Yehova kumachepetsa kudwala ndi imfa ndipo kumapeŵetsa kutaikiridwa ndalama zambiri ndi zovuta zosalekeza, kodi tileke kuthira mwazi odwala ambiri?”
Awo amene amakana kuthiridwa mwazi pachifukwa cha umboni umenewo adzakhala akuchitanso mogwirizana ndi malangizo a Mlengi wathu.