Dzina la Mulungu
“Kusiyapo ngati Yehova amanga nyumba, omangawo agwira ntchito pachabe.” Ndimo mmene malembo Achilatini ameneŵa amaŵerengedwera. Mawu amenewo akuchokera pa Salmo 127:1 m’Baibulo, ndipo ngowonadi: Kuyesayesa kulikonse kumene kuli kopanda dalitso la Yehova potsirizira pake kumakhala kwachabe.
Malembowo, a deti la 1780, akupezeka panyumba ina mu Colombo, Sri Lanka, ndipo ngodziŵika chifukwa chakuti ali ndi dzina la Mulungu, Yehova. (Onani chithunzithunzi.) M’zaka mazana akale dzina limenelo linagwiritsiridwa ntchito mofala. Kaŵirikaŵiri linazokotedwa panyumba zaboma, matchalitchi, ngakhale pamakobiri. Amishonale anagwiritsira ntchito dzina la Mulungu pamene analalikira za m’Baibulo kumaiko akutali, zimene mosakayikira zinachititsa kulembedwa kwa malembowo m’Sri Lanka.
Koma lerolino zinthu nzosiyana chotani nanga! Ali oŵerengeka chabe odzitcha kuti Akristu amene amasamala za dzina la Mulungu. Akatswiri ena amasulizadi Mboni za Yehova chifukwa cha kuligwiritsira ntchito kwambiri. Chifukwa ninji? Malinga nkunena kwa ena, chifukwa chakuti matchulidwe ake a Chihebri sakudziŵika bwino kwambiri. Koma kodi ndianthu angati amene amadziŵa matchulidwe oyambirira enieni Achihebri a dzina la Yesu? Komabe, dzina lake limagwiritsiridwa ntchito padziko lonse ndipo limalemekezedwa.
Kwa Yesu, dzina la Mulungu linali lofunika koposa. Anatiphunzitsa kupemphera motere: “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Ndipo imfa yake ili pafupi, iye anati kwa Mulungu: “Ndalionetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa ine m’dziko lapansi.” (Yohane 17:6) Akristu owona ali otsatira mapazi a Yesu. Kodi nawonso sayenera ‘kuonetsa dzina la Mulungu’? Mboni za Yehova zimatero, ndipo Yehova amadalitsa “nyumba” yawo. Kwa iwo salmo ili nlowona: “Odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”—Salmo 144:15.