“Tiyeni Tiyambe Taŵerenga Kwambiri Tisananyozere”
IZO nzimene munthu wina wa ku New Zealand ananena ponena za Nsanja ya Olonda, magazini amene mukuŵerenga. Ponena za nkhani yonena za galeta lakumwamba la Mulungu lofotokozedwa mu Ezekieli chaputala 1, munthuyo analemba kuti:
“Chilichonse cha zamoyo zinayi zimenezi, kapena akerubi, chinali ndi mapiko anayi ndi nkhope zinayi. Zinali ndi nkhope ya mkango, yoimira chilungamo cha Yehova; nkhope ya ng’ombe, yoimira mphamvu ya Mulungu; nkhope ya chiwombankhanga, yotanthauza nzeru zake; ndi nkhope ya munthu, yosonyeza chikondi cha Yehova.
“Nditaŵerenga zimenezi mobwerezabwereza, mtima wanga unakhudzidwa kwambiri. Misozi inadzala m’maso mwanga, ija yachimwemwe. Malingaliro omwe ndinakhala nawo panthaŵi yomweyo anali akuti, ‘Muyenera kukhala wokongola ndi wabwino chotani nanga, Yehova!’ Malingaliro atsopano ameneŵa kulinga kwa Yehova Mulungu ameneyu amene ndatonza kwazaka zambiri akundidabwitsa, pokhala munthu wakudziko mmene ndilirimu. Ndikuti ‘zikomo’ kwa Mboni za Yehova, ndipo kwa ambiri onga ine, ndikuti, ‘Tiyeni tiyambe taŵerenga kwambiri tisananyozere.’”