Usiku Wofunika Kukumbukira
PATSIKU lokumbukiridwa zaka zoposa 3,500 zapitazo, Yehova Mulungu analamula Aisrayeli ogwidwa ukapolo mu Igupto kupha mwana wa nkhosa ndi kuwaza mwazi wake pamphuthu za nyumba zawo. Usiku womwewo, mngelo wa Mulungu anapyola nyumba zoikidwa chizindikiro mwanjira imeneyi koma anapha ana oyamba kubadwa m’nyumba za Aigupto onse. Pamenepo Aisrayeli anamasulidwa. Chiyambire pamenepo, padeti la chochitika cha chaka ndi chaka chimenecho, Ayuda anakhala akukumbukira Paskha.
Mwamsanga Yesu Kristu atamaliza kukumbukira Paskha wake wotsiriza ndi atumwi ake, anayambitsa chakudya chimene chikakhala chikumbukiro cha imfa yake ya nsembe. Iye anapatsa atumwi ake okhulupirikawo mkate nanena kuti: “Tengani, idyani; ichi ndithupi langa.” Ndiyeno anawapatsa chikho cha vinyo ndipo anati: “Mumwere ichi inu nonse, pakuti ichi ndi mwazi wanga wa pangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.” Yesu ananenanso kuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.” (Mateyu 26:26-28; Luka 22:19, 20) Chotero Yesu analamula otsatira ake kusunga chochitika cha imfa yake chimenechi.
Mboni za Yehova zikukupemphani mwachikondi kuti mudzagwirizane nazo pa Chikumbutso chimenechi cha imfa ya Yesu. Mungathe kufika pa Nyumba Yaufumu yapafupi ndi kwanuko. Onanani ndi Mboni za kwanuko kuti mudziŵe nthaŵi yake yeniyeni ndi malo. Deti la chochitikacho mu 1994 ndilo pa Loŵeruka, March 26, mkate ndi vinyo zidzaperekedwa dzuŵa litaloŵa.