Lipoti la Olengeza Ufumu
Anatsatira Chikumbumtima Chake Chophunzitsidwa ndi Baibulo
MFUMU Davide wa Israyeli anapemphererera chithandizo cha Yehova pamene ananena kuti: “Koma ine ndidzayenda m’ungwiro wanga; mundiombole, ndipo ndichitireni chifundo.” (Salmo 26:11) Mulungu anamchitira chifundo chifukwa chosunga umphumphu wake. Yehova anadalitsanso Yesu chifukwa chakuti anachita chifuniro cha Atate wake wakumwamba, ndipo Iye anadalitsa wachichepere wa ku Colombia amene anatsatira chikumbumtima chake chophunzitsidwa ndi Baibulo ndi kutsimikiza mtima kuchita chifuniro cha Mulungu. Mnyamata ameneyu akusimba kuti:
“Pamene ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, nkuti ndili wophunzira pa sukulu Yachikatolika. Komabe, chikumbumtima changa chinandivutitsa pamene ndinapezeka pa Misa, chotero ndinapita kwa mkulu wa sukuluyo (yemwe anali wansembe), phungu wopereka chilangizo, ndi mtsogoleri wa kagulu kanga ndi kumpempha kuti ndiloledwe kusapezeka pa Misa. Ngakhale kuti ndinaloledwa, ena anayesa kundikakamiza kupezekapo. Chitsenderezocho chinawonjezereka mwamsanga pambuyo pa kubatizidwa kwanga monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Bambo wanga anandiopseza kuti adzandithamangitsa pa’nyumba ngati ndichotsedwa sukulu. Iwo anali kufuna kuti ndidzapite ku yunivesite ndi kugwira ntchito yaukatswiri.
“Mkulu wa sukuluyo anapereka machenjezo mobwerezabwereza kwa aliyense amene alephera kusunga malamulo Achikatolika. Pamene inafika nthaŵi ya Misa yoyamba ya chaka, ndinabisala kufikira itatha. Ndiyeno ndinapatsa mphunzitsi (wansembe) kope la brosha la School and Jehovah’s Witnesses ndi kumuuza kuti monga mmodzi wa Mboni za Yehova, sindingapezeke pa Misa. Iye anati: ‘Zili bwino kuti uyambe kufuna malo kusukulu ina.’ Ndinadziŵa kuti kuchotsedwa sukulu kukatanthauza kuthamangitsidwa panyumba ndi bambo wanga. Ngakhale zinali choncho, ndinapemphera kwa Yehova ndi kupitiriza kupereka umboni wokwanira kwa anzanga apasukulu.
“Nthaŵi ya tchuthi inafika. Ndiyeno, chitatha tchuthicho ndinabwerera kusukulu, ndipo inafikanso nthaŵi yochita Misa. Mkulu wa sukuluyo ndi ansembe ena anali kutsogolo m’chipinda cholambiriracho, ali okonzekera kumva kuulula machimo. Ndinatsala pang’ono kugonja chifukwa cha mantha. Ndinaloŵa mkatimo ndi kukhala pansi, koma chikumbumtima changa chinandivutitsa. Pamene anayamba kuimba, ndinalingalira kuti, ‘Kodi ndikuchita chiyani muno? Yehova ndiye Mulungu wanga. Sindingakhale wamantha ndi kumunamiza. Sindingamgwiritse mwala. Sadzandisiya.’ Ndinapemphera kuti ndilimbe mtima. Ndiyeno, ndinatuluka m’chipinda cholambiriracho ndi kuima pamzera wa opita kukaulula machimo. Pamene ndinafika kwa mkulu wa sukuluyo, ndinamuuza kuti: ‘Aphunzitsi, sindinabwere kudzaulula machimo.’ Iye anati: ‘Ndinalingalira choncho.’ Ndinawauza kuti ndinali wofunitsitsa kuvutika ndi zotsatirapo zake ndipo chikumbumtima changa sichinandilole kuchita nawo Misa. Sindikanatha kuchita motsutsana ndi zinthu zimene ndinaphunzira m’Baibulo.
“Iwo anandiyang’ana dwi, namwetulira, nati: ‘Umandichititsa chidwi. Nonsenu Amboni muyenera kutichititsa chidwi. Kwa inu, Mulungu amakhala pamalo oyamba, ndipo ndinu okonzekera kumvera malamulo ake mosasamala kanthu za zimene zingachitike. Pitiriza kuchita zimenezi. Ukuchita bwino kwambiri. Ndikulakalaka kuti bwenzi Akatolika onse akanakhala ofanana nanu, akumasonyeza changu chotero ndi chikondi kwa Mulungu. Kuyambira tsopano kumka mtsogolo, uli wololedwa kusatenga mbali m’zochitika zathu zachipembedzo.’ Ndinali wosangalala chotani nanga! Yehova anadalitsa kutsimikiza mtima kwanga kumvera chikumbumtima changa chophunzitsidwa ndi Baibulo.
“Tsiku lotsatira mkuluyo anauza ophunzira kuti: ‘Zipembedzo zina zatiposa. Kodi nchifukwa ninji sitili ofanana nazo, achangu, okhala ndi chikondi chakuya kaamba ka Mulungu ndi chikhumbo cha kutumikira iye kuposa zina zonse? Zimenezi ndi zinthu zimene ziyenera kukhala m’mitima mwathu.’
“Pomalizira pake mphunzitsiyo anasamutsidwira ku Rome, ndipo mphunzitsi watsopanoyo anangonyalanyaza kusatenga mbali kwanga. Bambo wanga anachoka panyumba, nandisiya waufulu kukwaniritsa chonulirapo changa cha utumiki wa nthaŵi yonse pambuyo pomaliza maphunziro.”
Yehova anadalitsa mnyamata ameneyu amene anatsatira chikumbumtima chake chophunzitsidwa ndi Baibulo. Iye adzadalitsa mofananamo onse amene amafunafuna kuchita chifuniro chake.—Miyambo 3:5, 6.