“Mizu Imene Singazulidwe”
PAKATI pa zinthu zamoyo zazikulu koposa ndi zakale koposa pali mitengo ya sequoia ya ku California. Mitengo yozizwitsa yaitali imeneyi imafika pa msinkhu wa mamita 90 itakhwima ndipo ingakhale ndi moyo kwa zaka pafupifupi 3,000.
Ngakhale kuti maonekedwe a sequoia ali ochititsa mantha, dongosolo lake la mizu yosaoneka lilinso lochititsa chidwi. Mtengo wa sequoia uli ndi mizu yolukanalukana imene ingakute malo aakulu pafupifupi mahekita 1.2 kufikira 1.6. Dongosolo la mizu limeneli lokuta malo aakulu lili maziko olimba amene amagwira mtengowo ngakhale pamene kuli maliyambwe kapena mikuntho. Ndipo nkotheka kwa mtengo wa sequoia kuchirimika pa chivomezi chachikulu!
Mfumu Solomo anasankha dongosolo la mizu lolimba la mtengo monga fanizo mu umodzi wa miyambi yake. “Palibe munthu amene angakhazikike ndi kuipa,” iye anatero, “koma anthu abwino ali ndi mizu imene singazulidwe.” (Miyambo 12:3, The New English Bible) Inde, oipa aima pa malo osalimba. Chipambano chilichonse chimene amaoneka kukhala nacho chili chakanthaŵi chabe, pakuti Yehova akulonjeza kuti “chiyembekezo cha . . . oipa chidzawonongeka.”—Miyambo 10:28.
Limeneli ndi chenjezo kwa awo amene amadzitcha kukhala Akristu, pakuti Yesu ananena kuti ena sakakhala ndi “mizu” mwa iwo eni ndipo akakhumudwa. (Mateyu 13:21) Ndiponso, mtumwi Paulo analemba za anthu amene ‘akatengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso [chonama].’ (Aefeso 4:14) Kodi zimenezi zingapeŵedwe motani?
Monga momwedi mizu ya mtengo wa sequoia imakutira malo aakulu m’nthaka yachonde ya dziko lapansi, moteronso maganizo ndi mitima yathu zifunikira kuloŵa mwakuya m’Mawu a Mulungu ndi kutungamo madzi opatsa moyo. Zimenezi zidzatithandiza kukulitsa chikhulupiriro chozika mizu zolimba. Ndithudi, tidzayambukiridwa ndi ziyeso zonga chimphepo. Mwinamwake tingagwederedi, mofanana ndi mtengo, poyang’anizana ndi tsoka. Koma ngati chikhulupiriro chathu chili ndi maziko olimba, tidzakhaladi ndi “mizu imene singazulidwe.”—Yerekezerani ndi Ahebri 6:19.