Baibulo—Kodi Phindu Lake Lenileni Nlotani?
“BAIBULO ndi chinsinsi, ndi buku lomwe linalembedwa kuti lisamvetsetsedwe,” akutero mwininyumba wina. Winanso akuti: “Ndikudziŵa kuti Baibulo ndi buku lofunika kwambiri, koma sindidziŵa zambiri ponena za ilo. Nlovuta kumva.”
“Akristu ambiri amadziŵa . . . zochepa ponena za Baibulo,” inatero The Toronto Star. Mkazi wina Wachikatolika ananena kuti: “Ndimamva bwino ndikakhala ndi Baibulo. Limandidzetsera mtendere wamaganizo.” “Baibulo lili ngati compass imene imatsogolera munthuwe kupyola m’nyanja yoŵinduka, yamafunde ya moyo kumka kumalo achisungiko,” akutero msodzi wina. Malinga ndi kunena kwa Mhindu wina wakale, “Baibulo lili Mawu a Mulungu ndipo ndi mphatso kwa mtundu wa anthu ndi mankhwala a matenda auzimu.”
Malingaliro onena za phindu lenileni la Baibulo ali ambiri ndi osiyanasiyana. Komabe, kodi phindu lake lenileni nlotani?
Baibulo ndi buku lokha lomwe lilipo limene lili lofunika koposa ndi lofalitsidwa kwambiri. M’masamba ake muli mayankho a mavuto aakulu koposa amene munthu wakumana nawo kapena amene adzayang’anizanabe nawo. Kugwira ntchito kwa uphungu wake nkosalingana ndi kwina kulikonse. Miyezo ya makhalidwe imene limachirikiza njopambana. Uthenga wake ngwamphamvu ndi wopindulitsa. Buku limeneli la phindu losayerekezereka liyenera kutengedwa pamashelufu athu ndi kuŵerengedwa mosamalitsa ndi kupendedwa mwakuya.
Tingatsegule Baibulo ndi chidaliro chachikulu chakuti lili lolondola, lodalirika, ndi loona kotheratu. Zochitika za m’mbiri zolembedwamo zimatsimikiziridwa ndi mbiri ya dziko. Mobwerezabwereza, zopezedwa ndi ofukula m’mabwinja zimachitira umboni kuti Baibulo limanena zenizeni ndipo nloona. Kunena zinthu mosabisa kwa alembi a Baibulo 40 kapena kuposapo kumawasonyeza kukhala amuna oona mtima ndi okhulupirika. Kugwirizana kwa zamkati mwa Baibulo kumasonyeza kuti silinachokere kwa munthu. Zochitika zolembedwamo zili zenizeni. Anthu amene limanena za iwo ali enieni. Malo ndi madera amene limatchula ali enieni. Ndiponso, Baibulo lili ndi maulosi apadera amene mosatsutsika amadziŵikitsa Yehova Mulungu kukhala Mlembi wa Baibulo.—2 Petro 1:21.
Mlangizi wathu Wamkulu anatsimikizira kuti chidziŵitso chonena za chifuniro chake ndi zifuno zake chikapezeka kwa awo amene anafuna kuchidziŵa. Kwenikweni, Yehova amatiuza momvekera bwino kuti chili chifuniro chake kuti anthu amtundu uliwonse aphunzire Mawu ake “nafike pozindikira choonadi.” (1 Timoteo 2:3, 4; Miyambo 1:5, 20-33) Chimenechi chili chimodzi cha zinthu zofunika koposa chimene tingachite ndi moyo wathu. Ndicho chitokoso chimene tiyenera kuyang’anizana nacho. Akristu oyambirira anazindikira zimenezi. Mmodzi wa iwo anasonkhezeredwa kunena kuti: “Ndipo ichi ndipempha, kuti chikondi chanu chisefukire chiwonjezere, m’chidziŵitso, ndi kuzindikira konse; kuti [mukatsimikizire zinthu zofunika koposa, NW].”—Afilipi 1:9, 10; Akolose 1:9, 10.
Baibulo lili njira yaikulu ya Mlengi yofotokozera chifuniro ndi chifuno chake ku banja laumunthu, ndipo limalongosola mmene ife patokha timaloŵera m’chifuno chimenecho. Mkati mwake mwalembedwa zochitika zakale, ndipo limapereka chithunzi choonekera bwino cha mtsogolo. Baibulo limasonyeza chiphunzitso cholondola ndi kutiwongolera ponena za zimene tiyenera ndi zimene sitiyenera kukhulupirira. (Machitidwe 17:11; 2 Timoteo 3:16, 17) Limapereka malamulo a mkhalidwe amene munthu ayenera kutsatira, ndipo limatsogolera anthu m’njira ya chipambano ndi chimwemwe. (Mateyu, machaputala 5 mpaka 7) Limagogomezera Ufumu wa Mulungu monga chiyembekezo chokha cha mtundu wonse wa anthu ndipo limasonyeza mmene boma lake liliri chipangizo choyeretsera dzina lake ndi kulemekezera uchifumu wake. Baibulo limafotokoza njira imene tifunikira kulondola kuti tikhale ndi unansi wathithithi ndi wachikondi ndi Mpatsi wathu wa Moyo, Yehova.
Ndiponso, Baibulo ndilo buku lokha limene lidzakutsogolerani ku mphotho yaikulu koposa imene mtundu wa anthu udzalandira—moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso monga anthu angwiro. (Aroma 6:23) Mwana wobadwa yekha wa Yehova akutiuza kuti: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Ndithudi, buku lomwe lili ndi phindu lalikulu motero liyenera kutisonkhezera kuphunzira zimene tiyenera kuchita kuti tipeze mphotho ya moyo wosatha. Baibulo ndi buku lomwe linalembedwa kuti limvetsetsedwe, monga momwe nkhani yotsatira idzasonyezera.