Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 11/1 tsamba 32
  • Kodi Nchifukwa Ninji Oipa Amapambana?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchifukwa Ninji Oipa Amapambana?
  • Nsanja ya Olonda—1994
Nsanja ya Olonda—1994
w94 11/1 tsamba 32

Kodi Nchifukwa Ninji Oipa Amapambana?

“OIPA akhaliranji ndi moyo?” Funso limeneli linafunsidwa kale kwambiri ndi Yobu wokhulupirika, ndipo labwerezedwa nthaŵi zambiri kuyambira m’tsiku lake. Mosakayikira lili m’maganizo mwa anthu ambiri a ku Yugoslavia wakale (onga mkazi wosonyezedwa pachikuto chathu) amene ali ndi chisoni kaamba ka amene akuvutika m’nkhondo yankhalwe. Kodi nchifukwa ninji anthu oipa amapulumuka ndipo ngakhale kupambana? Monga momwe Yobu ananenera, kaŵirikaŵiri “nyumba zawo sizitekeseka ndi mantha, ngakhale ndodo ya Mulungu siiwakhalira.” ​—Yobu 21:7, 9.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti kutumikira Mulungu, kukonda mnansi wako, ndi kupeŵa kuchita choipa kulibe phindu? Kutalitali! Baibulo limatipatsa kaonedwe kabwino ka zinthu pamene limati: “Usalimbike kuti upose oipa kapena kutsanzira ochita choipa. Pakuti monga udzu umauma msanga, ndi kufota monga msipu wa ngululu. Khulupirira AMBUYE nuchite chabwino.”​—Salmo 37:1-3, The New English Bible.

Inde, kupambana kooneka kwa oipa kuli kwa kanthaŵi chabe. Kwenikweni, miyoyo yawo njaifupi kwambiri, pamene kuli kwakuti awo amene amatumikira Mulungu ali ndi chiyembekezo chabwino koposa kaamba ka mtsogolo. Posachedwa, lonjezo la Mulungu lidzakwaniritsidwa lakuti: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:4) Ali olungama okha, osati oipa, amene adzakhalako panthaŵiyo. Ha, ndi chilimbikitso chotani nanga chakuti tiyandikire kwa Mulungu ndi kuphunzira kuchita chifuniro chake, mosasamala kanthu za kuipa kwa awo otizinga!

Ngati mungafune chidziŵitso chowonjezereka kapena ngati mungakonde kuti wina adze kudzachita nanu phunziro Labaibulo lapanyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yoyenera pandandanda ya patsamba 2.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena