Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 8/1 tsamba 8
  • Kufikira Midzi Yakutali ya Greenland

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufikira Midzi Yakutali ya Greenland
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Gawirani Magazini mu Utumiki Wanu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!—Magazini Apanthaŵi Yake a Chowonadi
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Zimene Akazi Ayenera Kudziŵa Ponena za Kansa ya Maŵere
    Galamukani!—1994
  • Zimene Mungachite Ngati Mwapezeka ndi Khansa ya M’mawere
    Galamukani!—2011
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 8/1 tsamba 8

Olengeza Ufumu Akusimba

Kufikira Midzi Yakutali ya Greenland

KWA zaka makumi ambiri Mboni za Yehova zagwiritsira ntchito magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! polalikira uthenga wabwino. Magazini ameneŵa amatamanda nzeru ya Yehova monga momwe yalongosoledwera m’Mawu ake, Baibulo. Amayang’anira zochitika za dziko zimene zimagwirizana ndi ulosi wa Baibulo, ndipo amapereka malangizo abwino a m’Baibulo pa mavuto amakono.​—Yakobo 3:17.

Mu 1994, Mboni ku Greenland zinayesayesa mwapadera kugaŵira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kwa anthu ambiri. M’chilimwe, zinapanga makonzedwe a kukafikira midzi ina yakutali kwambiri ya ku Greenland. Kagulu ka olengeza Ufumu kanayenda ulendo wa paboti wa makilomita oposa 4,000 kumka kugombe la kummwera la Qaanaaq (Thule), akumafikira midzi ina ya kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi. Ulendo wawo unatenga masabata asanu ndi aŵiri. Kugombe lakummaŵa, Mboni ziŵiri zokwatirana zinafika pa mudzi wina ku Ittoqqortoormiit ndipo kwa nthaŵi yoyamba zinalalikira uthenga wabwino m’mudzi wonsewo.

Kumayambiriro kwa chakacho, m’mwezi wa April, makope 7,513 a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! anagaŵiridwa kwa anthu a ku Greenland. Zimenezo zikutanthauza kuti, pa avareji, aliyense wa ofalitsa Ufumu 127 anagaŵira magazini 59​—magazini 1 pa nzika 7 zilizonse. Mwezi umenewo, Galamukani! anali ndi mipambo ya nkhani zakuti “Kansa ya Maŵere​—Nkhaŵa ya Mkazi Aliyense.” Mboni ina, imene inagaŵira magazini 140, inasiyira makope a Galamukani! ameneyo kwa mtolankhani wa pa wailesi yakanema wina. Patapita masiku angapo, programu ina ya nkhani za pa wailesi yakanema inasonyeza nkhani za kansa ya maŵere. Mtolankhaniyo anasonyeza magaziniwo pa wailesi yakanema, akumasonyeza masamba angapo pamene anali kuyamikira mmene anatembenuzidwira m’Chigirinilande. Anasonyezanso za malingaliro othandiza operekedwa mu Galamukani! monga njira yotetezerera thanzi la munthu.

Mboni yachikazi imene inagaŵira magazini kwa mtolankhaniyo inafunsidwa pa programu imodzimodziyo ya pa TV. Iyo inayankha mafunso ambiri okhudza Mboni za Yehova ndipo inafotokozanso ponena za mkupiti waukulu wa kugaŵira magaziniwo mweziwo. Inafotokozanso ponena za nzeru yeniyeni yopezeka m’Baibulo ndi kusonyeza kuti malangizo abwinowo angatithandize kulimbana ndi mavuto amasiku ano.

Programuyo inamalizidwa ndi kufunsa pulezidenti wamkazi wa Greenlandic Cancer Society. Iye anati anali asanaonepo mfundo zopatsa chidziŵitso zoterozo pankhaniyi m’chinenero chake. Ndiyeno anapempha onse amene ali ndi chidwi pankhani ya kansa ya maŵere kuŵerenga nkhani za mu Galamukani! Anati panali chifukwa chabwino chothokozera Mboni za Yehova chifukwa cha luso lawo.

Monga momwe zilili ku Greenland, Mboni za Yehova padziko lonse zikupitiriza kulalikira uthenga wabwino ku “cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.” (Akolose 1:23; Machitidwe 1:8) Mwa kugwiritsira ntchito mabuku ofotokoza Baibulo, kuphatikizapo Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, akuthandiza anthu a mtundu uliwonse kulimbana ndi mavuto amakono ndiponso kuwapatsa chiyembekezo cha mtsogolo mwabwino kwambiri.

[Mapu patsamba 8]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Qaanaaq (Thule)

Ittoqqortoormiit

Nuuk (Godthåb)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena