Kuthira Mwazi Kupendedwanso
M’NYENGO yachisoni ino ya AIDS, ngozi yaikulu kopambana pa umoyo wa wodwala m’chipatala ingabisale m’chipinda cha opaleshoni. “Palibe njira imene tingachitisire mwazi kukhala wotetezereka kotheratu,” akutero Dr. Richard Spence, amene kwa zaka zoposa khumi, wakhala mkulu wa Center for Bloodless Surgery pa Cooper Hospital-University Medical Center ku Camden, New Jersey, U.S.A.
Nkosadabwitsa kuti chipatalacho chimachiritsa Mboni za Yehova zambiri, zimene kukana kwawo kuthiridwa mwazi kozikidwa pa Baibulo nkodziŵika bwino. (Levitiko 17:11; Machitidwe 15:28, 29) Komabe, odwala enanso amene sali Mboni amafikanso kuchipatala chimenecho, powopa ngozi za kuthira mwazi, zimene zimaphatikizapo kutenga hepatitis, AIDS, ndi matenda ena. “Kuwonjezeka kwa AIDS kwasonyeza kufunika kwa kupima mwazi,” ikutero Courier-Post Weekly Report on Science and Medicine. “Koma nthaŵi zina kupimako sikumapeza kanthu chifukwa chakuti munthuyo angakhale ndi kachirombo kamene sikanafike pausinkhu woonekera popima.”
Chifukwa cha ngozi zotero, chipatala cha Center for Bloodless Surgery chimagwiritsira ntchito njira zina m’malo mwa kuthira mwazi, kuphatikizapo kuthira wodwalayo mwazi wa iye mwini—njira imene Mboni zina zingavomereze pansi pa mikhalidwe ina.a Njira ina yochiritsira imaloŵetsamo kugwiritsira ntchito mankhwala amene amayambitsa kupangika kwa mwazi mwa wodwalayo. Ndiponso, msanganizo wina wopanga wogwira ntchito monga mwazi umagwiritsiridwa ntchito nthaŵi zina kusonkhezera kuperekedwa kwa oxygen popanda kuthira mwazi. “Mboni za Yehova zimafuna chisamaliro chamankhwala chabwino koposa,” akutero Dr. Spence, “koma zimafuna mankhwala ena m’malo mwa mwazi.”
Mboni za Yehova zimayamikira kwambiri chigwirizano ndi chithandizo chimene zimapatsidwa ndi madokotala amene amalemekeza zikhulupiriro zawo zachipembedzo. Chifukwa cha zimenezo, izo zalandira “chisamaliro cha mankhwala chabwino koposa” ndipo zasunga chikumbumtima choyera pamaso pa Yehova Mulungu.—2 Timoteo 1:3.
[Mawu a M’munsi]
a Kufotokoza kwatsatanetsatane kwa njira imeneyi ndi mbali zoloŵetsedwamo popanga chosankha chaumwini cha chikumbumtima kuli mu Nsanja ya Olonda ya March 1, 1989, masamba 30-1.