Pamene “Mphepo Imakhala Yopanda Ntchito”
“PAMENE munthu sadziŵa komwe kuli doko limene akufuna kupitako, mphepo imakhala yopanda ntchito.” Mawu ameneŵa, onenedwa ndi wanthanthi Wachiroma Lucius Annaeus Seneca, amasonyeza za choonadi chodziŵika kwa nthaŵi yaitali: Kuti moyo ukhale ndi chitsogozo, zonulirapo nzofunika.
Komabe, kaŵirikaŵiri moyo umakhala wopanda chifuno. Ambiri amakhutira ndi kupeŵa miyala ndi maphote a moyo watsiku ndi tsiku. Pokhala osakhazikika, amakhala ngati mafunde amene “amatengeka ndi mphepo ndi kuŵinduka nayo.” (Yakobo 1:6) Kwa anthu otero, “mphepo imakhala yopanda ntchito.”
Baibulo limapereka zitsanzo za awo amene anali ndi chonulirapo, akumakhala zitsanzo za Akristu amakono. Mose “anapenyerera chobwezera cha mphotho.” (Ahebri 11:26) Paulo analemba kuti: “Ndithamanga molunjika kulinga ku chonulirapocho kuti ndipeze mphotho.” Analimbikitsa okhulupirira anzake ‘kukhala ndi maganizo amodzimodziwo.’—Afilipi 3:14, 15, “Today’s English Version.”
Pokhala maso athu atalunjikitsidwa pa malonjezo a Baibulo, titsanziretu chikhulupiriro cha amuna amenewo okhala ndi chonulirapo.—Yerekezerani ndi Ahebri 13:7.