Ŵalitsani Kuunika Kwanu!
POMALIZIRA pake nthaŵi inafika yakuti mwamuna wokalambayo aone Mesiya wolonjezedwa! Mwa vumbulutso la Mulungu Simeoni anadziŵa kuti ‘sadzaona imfa, kufikira adzaona Kristu wake wa Yehova.’ (Luka 2:26) Koma zinali zokondweretsa chotani nanga pamene Simeoni analoŵa m’kachisi ndipo Mariya ndi Yosefe naika khandalo Yesu m’manja mwake! Anatamanda Mulungu, akumati: “Tsopano, Ambuye, . . . lolani ine, kapolo wanu, ndichoke mumtendere; chifukwa maso anga adaona chipulumutso chanu, . . . kuunika kukhale chivumbulutso cha kwa anthu a mitundu, ndi ulemerero wa anthu anu Israyeli.”—Luka 2:27-32; yerekezerani ndi Yesaya 42:1-6.
Yesu, kuyambira pa ubatizo wake pausinkhu wa zaka 30 kufikira pa imfa yake, anakhala “kuunika” kwa dziko. M’njira zotani? Iye anatulutsa kuunika kwauzimu mwa kulalikira za Ufumu wa Mulungu ndi zifuno Zake. Anavumbulanso ziphunzitso zonyenga zachipembedzo ndi kudziŵikitsa poyera ntchito zimene zinali zamdima. (Mateyu 15:3-9; Agalatiya 5:19-21) Chotero, Yesu anatha kunena molondola kuti: “Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi.”—Yohane 8:12.
Yesu anafa m’chaka cha 33 C.E. Kodi panthaŵiyo kuunika kunazima? Kutalitali! Akali padziko lapansi, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Muŵalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu.” (Mateyu 5:16) Moyenerera, imfa ya Yesu itachitika ophunzira ake anaŵalitsa kuunika kwawo.
Potsanzira Yesu, Akristu lerolino amatulutsa kuunika kwa Yehova mwa kuchita ntchito yolalikira. ‘Amayenda monga ana a kuunika,’ akumadzisonyeza kukhala zitsanzo zapadera pamoyo wachikristu.—Aefeso 5:8.