Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 6/15 tsamba 32
  • Anatumikira Yehova Modzichepetsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anatumikira Yehova Modzichepetsa
  • Nsanja ya Olonda—1996
Nsanja ya Olonda—1996
w96 6/15 tsamba 32

Anatumikira Yehova Modzichepetsa

“CHOFUNIKA kwenikweni si kumene mukutumikira koma amene mukumtumikira.” John Booth anakonda kwambiri kunena mawuwo, ndipo anawatsatira. Moyo wake padziko lapansi, umene unatha pa Lolemba, January 8, 1996, sunasiye chikayikiro konse ponena za amene iye anasankha kutumikira.

Monga mnyamata kalelo mu 1921, John Booth anali kufunafuna chifuno cha moyo. Anali kuphunzitsa Sande sukulu ku Dutch Reformed Church, koma sanafune kulandira maphunziro a kukhala wansembe chifukwa anaganiza kuti atsogoleri achipembedzo anali adyera. Pamene anaona pepala lolengeza nkhani yakuti “Mamiliyoni Amene Ali ndi Moyo Tsopano Sadzafa Konse,” sanazengereze kuodetsa mabuku omwe linalengeza. Atachita chidwi ndi zimene anaŵerenga, posapita nthaŵi anali kumatchova njinga makilomita 24 kupita ku misonkhano ya Ophunzira Baibulo, dzina la Mboni za Yehova panthaŵiyo. Anabatizidwa mu 1923 nayamba kulalikira kunyumba ndi nyumba m’chigawo cha Wallkill, New York, kumene banja lakwawo linali ndi famu ya ng’ombe za mkaka.

Mbale Booth anayamba utumiki wanthaŵi zonse mu April 1928. Analalikira m’gawo lakwawo ndi kumidzi ya Kummwera, akumasinthanitsa mabuku a Baibulo ndi chakudya ndi pogona. Anapirira molimba mtima zowopsa monga eni nyumba zophikira moŵa wosaloledwa onyamula mfuti, amene mmodzi wa iwo anawombera mpainiya mnzake wa John Booth namvulaza. Mu 1935, Mbale Booth anaikidwa kukhala woyang’anira woyendayenda nayamba kumachezera mipingo ndi timagulu tating’ono m’dziko lonselo. Analinganiza misonkhano yaikulu ndi kuthandiza abale ndi alongo kulimbika mosasamala kanthu za chitsutso. Kulimbana ndi magulu achiwawa, kuima m’khoti, ndi kuponyedwa m’ndende zinakhala zinthu zachizoloŵezi kwa Mbale Booth. “Pangafunike buku kuti ndifotokoze zonse zochitika panthaŵi ija zosangalatsa,” analemba motero panthaŵi ina.

Mu 1941, Joseph F. Rutherford, pulezidenti wa Watch Tower Society panthaŵiyo, anatumiza Mbale Booth kukagwira ntchito ku Kingdom Farm, pafupi ndi Ithaca, New York. Kumeneko anatumikira mokhulupirika zaka 28. Chikondi chake cha utumiki chinali chosazirala, anakondwa zaka zambiri kuyanjana ndi ophunzira zikwi zambiri a Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower yophunzitsa amishonale, imene inali pa Kingdom Farm imeneyo mpaka 1961. Mu 1970, Mbale Booth anapemphedwa kukatumikira ku Watchtower Farms ku Wallkill, New York, ndipo motero anapezeka kudera limodzimodzi limene anayambirako upainiya zaka ngati 45 kalelo.

Mu 1974, Mbale Booth anaikidwa kukhala wa Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ku Brooklyn, New York. Anatumikira mokhulupirika pamalo amenewo kufikira imfa yake ali ndi zaka 93 zakubadwa. John Booth anakondedwa chifukwa cha umunthu wake wachikristu wa kudzichepetsa kwambiri ndi kukoma mtima. Kufikira pamene thanzi lake ndi nyonga zinamchepera, anali kulalikira mokhulupirika kunyumba ndi nyumba ndi m’makwalala a mzinda.

Pamene aja amene anatumikira naye akulira maliro a imfa yake, akupezabe chitonthozo m’lonjezo la Baibulo lonena za Akristu odzozedwa otero, kuti amaukitsidwira kumoyo wakumwamba ndi kuti “ntchito zawo zitsatana nawo pamodzi.” (Chivumbulutso 14:13; 1 Akorinto 15:51-54) Amenewotu ndi malo atsopano, koma ndi amene John Booth adzatumikiramo Yehova kosatha!

[Chithunzi patsamba 32]

John Booth 1903-1996

[Chithunzi patsamba 32]

HERALD-AMERICAN, ANDOVER 1234

76 Jehovites Jailed in Joliet

[Mawu a Chithunzi]

Chicago Herald-American

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena