Magazini Amene Amakhudza Mtima
MAGAZINI osaŵerengeka amafalitsidwa padziko lonse kuti akhutiritse njala ya chidziŵitso kapena ya kusanguluka ya woŵerenga.
Kodi nchiyani chimene chimachititsa magazini amene mwagwirawa kukhala apadera kwambiri? Kalata yotsatira, imene inafika ku ofesi yanthambi ya Watch Tower Society ku Germany, ingapereke yankho:
“Zikomo kwambiri, abale okondedwa, kaamba ka kuyesayesa kwanu ndi ntchito yanu. Pamene ineyo ndi ana anga aamuna aŵiri tinabwerako ku msonkhano, ngakhale kuti nthaŵi inali 9:30 p.m., ndinayenerabe kumvetsera Nsanja ya Olonda yatsopano [pa kaseti]. Pamene ndinali kutsuka mbale, ndinayamba kumvetsera nkhani yophunzira yoyamba (April 1, 1995). Ndinalingalira kuti ndiyenera kuimvetseranso, chotero ndinaleka ntchito yanga kukhichini ndi kuŵerenga nkhaniyo [“Ndinu Wamtengo Wapatali Pamaso pa Mulungu!”] mu Nsanja ya Olonda motsagana ndi tepi. Inandikhudza mtima, makamaka ndime yachinayi ndi yachisanu. Ndiyeno misozi inayamba kugwa—koma osati kwa nthaŵi yaitali. Ndikuyamikira Yehova kuti ndili moyo ndipo ndili mmodzi wa anthu ake ndi kuti ineyo, limodzinso ndi ena ambiri, tikudziŵikitsa dzina lake. Palibedi chifukwa chomvera kukhala wopanda pake. Mzimu wa Yehova uli ndi anthu ake. Tonsefe tipiriretu ndi kuima mosagwedera m’chikhulupiriro, mogwirizana. Moni wachikondi chachikristu, ndine mlongo wanu m’chikhulupiriro.”
Nsanja ya Olonda simangopereka chidziŵitso chokha. Imakhudza mtima wa oiŵerenga ndi kukhutiritsa njala yawo ya chakudya chauzimu ndi chilimbikitso cha panthaŵi yake. Inde, Nsanja ya Olonda imapereka “zakudya panthaŵi yake.”—Mateyu 24:45.