Kodi ndi Ayani Amene Adzakhala Alaliki?
PAMSONKHANO wa Bungwe la Matchalitchi la Dziko Lonse zaka 40 zapitazo, mamembala ake analimbikitsidwa “kudzimangira m’chiuno ndi mzimu wakulalikira” ndi kuphunzitsa anthu awo “kumka namakalalikira.” Zaka zisanu pambuyo pake John A. O’Brien, mtsogoleri wa chipembedzo chachikatolika, analemba za kufunika kwa kupeza ophunzira atsopano “mwa kumka kwa iwo” ndipo osati chabe “mwa kungokhala m’nyumba zathu.” Ndiponso mu January 1994, Papa John Paul II anatero kuti ino “sinthaŵi yochita manyazi ndi Uthenga Wabwino, ndi nthaŵi ya kuulalikira pamadenga anyumba.”
Mwachionekere ziitano zakamodzikamodzi zimenezi za alaliki zimafikira pa makutu ogontha. Nkhani ina mu nyuzipepala ya ku Australia Illawarra Mercury inati: “Akatolika otchuka a ku South Coast sali ofunitsitsa kutsanzira njira ya Mboni za Yehova yosonyezera chikhulupiriro chawo.” Munthu wina anatero kuti changu cholalikira “simbali yamaganizo a Mkatolika.” Winanso anagamula kuti: “Nkwabwino kuti tchalitchi chidzitukule koma osati mwa kumagogoda pamakomo. Mwinamwake kupyolera mwa masukulu kapena kutumiza makalata zingakhale bwinopo.” Ngakhale mbusa wamkulu pa tchalitchi chapamalopo sanali wotsimikizira za mmene akanafotokozera mawu a Papawo. “Tiyenera kulimbikitsa anthu kukhala ndi moyo molingana ndi Uthenga Wabwino umene audziŵa kupyolera m’moyo wa iwo eni,” iye anatero. “Kaya zimenezo zikutanthauza kugogoda pamakomo iyo ndi nkhani ina.” Mutu wa nkhani ya m’nyuzipepalayo unazimanga bwino zonse pamodzi m’mawu awa: “Akatolika salabadira chiitano cha Papa cha kulalikira.”
Mosasamala kanthu za kulephera kwa Dziko Lachikristu kukalalikira, Mboni za Yehova zoposa mamiliyoni asanu zikumvera lamulo la Yesu lakuti: “mukani, phunzitsani anthu amitundu yonse.” (Mateyu 28:19, 20; yerekezerani ndi Machitidwe 5:42.) Kulalikira kwawo kwa khomo ndi khomo kukuchitidwa tsopano m’maiko oposa 230. Uthenga umene amalalikira ndi wodalirika, umagogomezera malonjezo odabwitsa a Baibulo ponena za mtsogolo. Bwanji osalankhula nawo nthaŵi ina pamene afika?