Kutsutsa Zinenezo ku France
MBONI ZA YEHOVA ku France posachedwapa zinanenezedwa kwambiri. Poona ngozi zomwe zipembedzo zotsata munthu zinadzetsa ku Europe ndi Japan, ofalitsa nkhani anafalitsa mabodza ponena za Mboni. Anazifotokoza molakwika kuti ndizo limodzi la magulu otsata munthu aakulu kopambana ndipo angozi koposa.
Poyesetsa kuwongolera zinthu, Mboni za Yehova zinafalitsa trakiti limene linayankha mafunso onga awa: Kodi Mboni za Yehova ndani? Kodi ndi Akristu? Kodi amalandira thandizo lamankhwala? Kodi nchifukwa ninji amayenda kukhomo ndi khomo? Kodi ndalama za ntchito yawo zimachoka kuti? Kodi ndi motani mmene Mboni za Yehova zimathandizira anthu?
Trakiti lopereka chidziŵitsolo m’Chifrenchi linali ndi mutu wakuti Mboni za Yehova—Zimene Muyenera Kudziŵa. Kuti ziligaŵire kwa anthu ambiri ndithu, izo zinalinganiza mkupiti. Kuyambira pa May 13 mpaka pa June 9, 1996, makope oposa mamiliyoni asanu ndi anayi anagaŵidwa.
Ambiri anakondwera nalo trakiti limeneli, kuphatikizapo akuluakulu a boma. “Kuneneza Mboni za Yehova kumene akuchitaku kwandinyansa kwambiri,” analemba motero mwamuna wina wa m’konsolo ataŵerenga trakitilo. “Nthaŵi zambiri ndimayamikira mkhalidwe wothandiza ndi wopanda dyera wa ntchito yanu.” Ataona trakitilo, wa m’Nyumba ya Malamulo ya Ulaya yense analemba kuti: “Anthu ochuluka akudziŵa bwino lomwe kusiyanitsa gulu la Akristu limene inu mulimo ndi magulu otsata munthu.”
Ku Brittany Mboni ina inapereka trakitilo kwa wansembe wina, amene analilandira pomwepo. “Ndikukuthokozani pazimene mukuchita,” anatero wansembeyo. Kenako anawonjezera kuti: “Anthu anga ndimawalimbikitsa kuti azikulandirani m’nyumba zawo ndi kukupangirani khofi. Mungauzenso ndi amene mukumana nawo kuti munafikanso kunyumba kwanga. Ndikufunanso kukuuzani kuti ndimakonda kuŵerenga mabuku anu.”
Mwamuna wina wachiprotesitanti ku Alsace anapempha phunziro la Baibulo mwa kulembera Watch Tower Society atalandira trakitili. Iye analemba kuti: “Pokhala nditasiyiratu kudalira tchalitchi changa, ndikuyembekezera kuyambiranso bwinobwino mwauzimu.” Ngakhale azineneza nthaŵi zina, Mboni za Yehova ku France—ndipo kungoti mbali zonse za dziko—zikupitirizabe kuthandiza anthu kufika pakukhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha zifuno za Mulungu, monga momwe Baibulo lazilongosolera.—2 Timoteo 3:16, 17.