“Ngale za Choonadi”
“Ngale za choonadi.” Umu ndimo mmene kalata imene inatumizidwa kunthambi ya Mboni za Yehova ku Nigeria inatchulira magazini aŵiri apadera. Wolembayo, mnyamata, akufotokoza kuti:
“Ndikukulemberani kuti ndikuthokozeni kwambiri chifukwa cha khama lanu pokhudza pafupifupi mbali zonse za moyo watsiku ndi tsiku kupyolera m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!
“Ndili ndi zaka 17. Chaka chatha nyumba ya wailesi kwathu kuno inakonza mpikisano wolemba nkhani yamutu wakuti ‘Chikondi Sindiko Kugonana Kokha—AIDS Ilikodi.’ Nkhani iliyonse inayenera kukhala ndi mawu osachepera pa 400. Wolemba nkhani yabwino kwambiri anali kudzafupidwa 1000 naira [$12.50, U.S.]. Ananena kuti anthu alembe nkhaniyo osati chabe kuti apeze mphoto, koma kutinso aphunzirepo kanthu. . . .
“Ndinapeza chidziŵitso chonena za AIDS m’magazini onse aŵiri. Nkhani zachikondi zinalimo zambirimbiri. Ndinatenga mfundo zanga m’Galamukani! ya August 8, 1978.
“Isanathe miyezi iŵiri chitumizire nkhani yangayo, anaiulutsa. Zinandidabwitsa kuti ndinakhala woyamba m’dera la Cross River ndi la Akwa Ibom!
“Chidziŵitso chonse chimene ndinagwiritsira ntchito ndinachipeza m’magazini omwewo. Nzokondweretsadi kuti Yehova akutipatsa chidziŵitso chapanthaŵi yake m’dziko losautsa ndi lodwalali. Akristufe timadziŵa kuti chikondi si kugonana kokha iyayi. Ndipo ukhondo ndi makhalidwe abwino amatitetezera kumatenda onga AIDS.
“Ndikukuyamikirani ndithu chifukwa cha ngale za choonadi zimene simutopa kutipatsa. Yehova azidalitsabe khama lanu pamene mukufalitsa magazini amtengo wapatali ameneŵa.”