Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 8/1 tsamba 32
  • Khoti Yapamwamba ya ku Connecticut Ichirikiza Zoyenera za Odwala

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khoti Yapamwamba ya ku Connecticut Ichirikiza Zoyenera za Odwala
  • Nsanja ya Olonda—1997
Nsanja ya Olonda—1997
w97 8/1 tsamba 32

Khoti Yapamwamba ya ku Connecticut Ichirikiza Zoyenera za Odwala

Pa April 16, 1996, khoti Yapamwamba ya ku Connecticut, U.S.A., inachirikiza mfundo yakuti Mboni za Yehova zili ndi ufulu wokana kulandira mwazi. Chigamulo chimenechi chinasinthitsa chiweruzo cha mlandu wina wakale.

Mu August 1994, Nelly Vega, mmodzi wa Mboni za Yehova, anayamba kukha mwazi kwambiri atabala mwana wake woyamba. Zoyesayesa zonse kuti aletse kukha mwaziko sizinaphule kanthu. Pamene Nelly anayamba kufooka, chipatala chinasankha kupempha khoti kuti liloleze kuika mwazi. Nelly anali atasaina kale khadi lokana mwazi kapena zinthu zina zilizonse zomwe asakanizako mwazi nthaŵi yonse imene adzakhale kuchipatalako, motero akumachotsera chipatalacho mlandu uliwonse ngati chinachake chingachitike chifukwa cha zosankha zakezo. Ngakhale zinali tero, chipatala chinanena kuti kukakamiza kuika mwazi kunali kuchitira zabwino mwana wobadwa kumeneyo, amene, malinga nkunena kwa chipatalacho, amafunikira kukhala ndi amayi akewo. Khoti yomwe inaweruza nkhaniyo inalinso ndi nkhaŵa, kusiyapo kukha mwazi kwake, anati Nelly ndi wachitsikana wathanzi, wofunika m’dziko. Motero, ngakhale kuti mwamuna wake ndiponso loya yemwe amamuimira pamlandu adayesetsa kupereka mfundo zotsutsa, khotiyo inaloleza ndipo anamuikadi mwazi.

Potsirizira pake, nkhaniyi inaperekedwa ku khoti Yapamwamba ya ku Connecticut. Kumeneko, bwalo linagamula kuti chipatala chinalanda zoyenera za Nelly. Chiweruzo chinati: “khotiyo inamvetsera nkhaniyo usiku, panthaŵi yangozi yomwe zinthu zonse zimachitidwa msangamsanga, choncho mbali zonse ziŵiri zinalibe nthaŵi yokwanira kuti ziganizire zoti nkunena.”

Kugamula mlandu kumeneku kwa khoti Yapamwamba ya ku Connecticut ndi kothandiza kwa anthu enanso omwe si Mboni za Yehova. “Nkofunika kwambiri kwa odwala onse omwe angakhale sakugwirizana ndi zosankha za dokotala wawo,” anatero Donald T. Ridley, loya wa Nelly. “Chiweruzochi chidzapangitsa kuti zipatala zisamanyalanyaze zoyenera za odwala, kaya zikhale zokhudzana ndi chipembedzo kapena ayi.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena