Kutunga “Madzi Akuya”
MWAMBI wa m’Baibulo umati: “Uphungu wa m’mtima mwa munthu ndiwo madzi akuya; koma munthu wozindikira adzatungapo.” (Miyambo 20:5) M’nthaŵi za Baibulo kunali kovuta kwambiri kutunga madzi kusiyana ndi mmene zilili m’maiko ambiri lerolino. Pamene Yesu analankhula ndi mkazi wachisamariya, iye anali kutunga madzi m’chitsime cha Yakobo, chitsime chozama mamita 23!—Yohane 4:5-15.
Monga momwe ikusonyezera Miyambo 20:5, kuzindikira kumene kumafunika kuti tipangitse munthu kutulutsa maganizo ake akuya ndi malingaliro a m’mtima mwake kuli kofanana kwambiri ndi kuyesayesa kumene kumafunika potunga madzi m’chitsime. Izi zilidi choncho pazochitika zambiri m’moyo. Mwachitsanzo, mwinamwake inu mukudziŵa anthu amene apeza chidziŵitso chochuluka ndi luso kwa zaka zambiri. Amenewa atakhala kuti sakufuna kupereka uphungu osafunsidwa, mungafunikire kuwapangitsa kuti akuuzeni. Mwa kusonyeza chidwi, kufunsa mafunso, ndi kufufuza mwaluso, mudzakhala mukumiza chitini chanu m’chitsime chakuya cha nzeru, kunena kwake titero.
Uphungu wa pa Miyambo 20:5 ngwofunikanso m’banja. Kaŵirikaŵiri, akazi amakonda kunena kuti: “Mwamuna wanga sandifotokozera malingaliro ake!” Mwamuna anganene kuti: “Mkazi wanga amangosiya kundilankhula!” M’zochitika zotero, kuzindikira kumafunika kuti mwamuna kapena mkazi atulutse maganizo amene ali pansi pa mtima wa mnzake wamuukwati. Mafunso aluso (Kodi panali zovuta zilizonse lero? Chinachitika nchiyani? Ndingakuthandizeni motani?) kaŵirikaŵiri angayambitse makambitsirano ochokera pansi pa mtima. Kusonyeza kuzindikira kotero kudzalimbitsa chomangira chaukwati, zimene zidzapindulitsa onse aŵiri mwamuna ndi mkazi wake.