Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 11/15 tsamba 3-4
  • Kodi Mukufunitsitsa Dziko Lolungama?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukufunitsitsa Dziko Lolungama?
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Tingatani Ngati Pachitika Zopanda Chilungamo?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • N’zotheka Kupirira Zinthu Zopanda Chilungamo
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kodi Zinthu Zopanda Chilungamo Zidzatha Padzikoli?
    Nkhani Zina
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 11/15 tsamba 3-4

Kodi Mukufunitsitsa Dziko Lolungama?

SITIMA ya pa madzi yamatabwa yokhala ndi milongoti itatu ndiponso yosanjikizana kamodzi yayandikira gombe limene tsopano likudziŵika ndi dzina lakuti Cape Cod, Massachusetts, U.S.A. Ogwira ntchito m’sitimamo ndi apaulendo 101 atopa ndi kukhala m’nyanja kwa masiku 66. Pofuna kuthaŵa kuzunzika chifukwa cha chipembedzo chawo ndiponso mavuto a zachuma, iwo ayenda ulendo wovutawu kudutsa Atlantic Ocean.

Pamene apaulendo a m’sitima imeneyi, Mayflower, akuona mtunda pa November 11, 1620, iwo ali ndi chiyembekezo chachikulu cha kuyambanso moyo wina watsopano. Amuna ambiri aakulu msinkhu mwa apaulendowo akusayina pangano lotchedwa Mayflower Compact, pofuna kuyala maziko a dziko labwino. M’pangano limeneli, iwo akukhazikitsa “malamulo olungama ndi osakondera” kaamba ka “ubwino wa anthu onse okhala m’derali.” Kodi chiyembekezo chawo cha dziko lamakhalidwe abwino ndi okomera aliyense​—dziko lolungama​—chakwaniritsidwa?

Ngakhale kuti pangano la Compact limene analisayina atakwera Mayflower likuonedwa kukhala limodzi mwa maziko a ulamuliro wa boma la America, chilungamo nchosoŵa ku America, monga momwedi zilili kuzungulira dziko lonse. Mwachitsanzo, talingalirani za mwamuna amene anawomberedwa ndi apolisi pamene anafuna kuthaŵa ataba katundu ndi kuwombera mwini sitolo. Iye anakasumira apolisiwo ndi mzinda wa New York ndipo anapata madola mamiliyoni ambiri malinga ndi chiweruzo chake.

Talingaliraninso za chitsanzo china. Pamene ophunzira anali kulemba mayeso a uloya pasukulu ya malamulo ku Pasadena, California, mmodzi wa iwo anagwidwa ndi matenda mwadzidzidzi ndipo anakomoka. Ophunzira aŵiri amene anali pafupi ndi iye mwamsanga anayamba kumtsitsimutsa mtima ndi mapapu mpaka pamene azaumoyo anafika pamalopo. Iwo anatha mphindi 40 akuthandiza mwamunayo. Koma pamene anapempha kuti awawonjezere nthaŵi kuti amalize mayesowo, woyang’anira mayesowo anakana.

Palinso nkhani ya kulanga apandu. Wofufuza kayendedwe ka chuma Ed Rubenstein akunena kuti: “Apandu ambiri sagwidwa. Ambiri amene amagwidwa saimbidwa mlandu. Apandu ambiri amamasulidwa. Mpandu amakayikira zakuti adzalangidwa, sakhala wotsimikiza.” Pogwiritsira ntchito chiŵerengero cha othyola nyumba, iye akunena kuti munthu woimbidwa mlandu wa kuthyola nyumba “adzapulumuka kuponyedwa m’ndende maulendo oposa 98 peresenti.” Kuchepa kwa chilango kumawonjezera upandu ndi anthu ovutika chifukwa cha upandu.​—Mlaliki 8:11.

M’maiko ambiri anthu olemera amangopitirizabe kulemera pamene kuli kwakuti anthu osauka amapitirizabe kuponderezedwa pazachuma. Kuponderezedwa kumeneku kumakhalapo pamene anthu alibe mwaŵi woti angatukule miyoyo yawo kapena ngakhale kudzipezera zofunika chifukwa cha khungu lawo, fuko, chinenero, chifukwa chakuti ndi amuna kapena akazi, kapena chifukwa cha chipembedzo chawo. Mwachitsanzo, malinga nkunena kwa magazini ya The New York Times, “pafupifupi mbali imodzi mwa mbali zinayi za chiŵerengero cha anthu mamiliyoni chikwi chimodzi m’dera la Ahindu ku South Asia​—ambiri a iwo amene amakhala ku India ndi ku Nepal​—amabadwa ndi kufa monga anthu odetsedwa.” Chotsatirapo chake nchakuti mamiliyoni a iwo amakanthidwa ndi umphaŵi, njala, ndi matenda. Iwo amatsenderezedwa kuyambira paukhanda wawo mpaka kufa kwawo.

Nanga bwanji ponena za kusoŵeka kwa chilungamo kumene anthu sangalamulire? Mukulingalira bwanji za ana obadwa opunduka​—akhungu, osokonezeka maganizo, kapena olemala? Kodi mayi angaleke kulingalira kuti palibe chilungamo pamene mwana wake abadwa wolemala kapena wakufa pamene amayi ena oyandikana naye ali ndi ana athanzi?

Mwachisoni, kupanda chilungamo nkofala, ngakhalenso zotsatirapo zake​—kuvutika kwakukulu ndi kusoŵa mtendere, chimwemwe, ndiponso chisangalalo. Pokwiya ndi kupanda chilungamo kumene aona kapena kuchitiridwa, ambiri amangoganiza zochita chiwawa, zimene zimangowonjezera kuvutika kwa anthu. Nkhondo zambiri zamenyedwa chifukwa cha nkhanza inayake.

Kodi nchifukwa ninji munthu walephera kudzetsa dziko lolungama? Kodi kulingalira za dziko lotero ndi loto chabe?

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Corbis-Bettmann

[Chithunzi patsamba 4]

Kusayina pangano lotchedwa Mayflower Compact

[Mawu a Chithunzi]

Corbis-Bettmann

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena