Olengeza Ufumu Akusimba
Chipiriro Chibweretsa Dalitso la Mulungu m’Malaŵi
YOSEFE anali mtumiki wokhulupirika wa Yehova. (Ahebri 11:22) Analinso munthu wopirira kwambiri. Ngakhale kuti anaperekedwa ndi abale ake, kaŵiri kugulitsidwa mu ukapolo, ndipo pambuyo pake kuikidwa m’ndende pa zifukwa zonama, Yosefe sanataye mtima. M’malo mwake, modekha anapirira zaka zosautsazo, nayembekezera dalitso la Yehova modzichepetsa.—Genesis 37:23-28, 36; 39:11-20.
Mofananamo lerolino, Mboni za Yehova m’Malaŵi zayembekezera modekha dalitso la Mulungu. Kwa zaka 26, Mboni zachikristu zimenezi zinapirira ziletso za boma, chitsutso chachikulu ndi nkhanza zochuluka. Koma chipiriro chawo chabweretsa mapindu!
Pamene chinzunzo chinayamba m’Malaŵi chakumapeto kwa 1967, munali pafupifupi ofalitsa Ufumu 18,000. Taganizirani za chisangalalo cha Mbonizo pamene zinamva kuti chaka cha utumiki cha 1997 chinayamba ndi chiŵerengero chatsopano cha ofalitsa 38,393—kuposa kuŵirikiza kaŵiri chiŵerengero chimene chinalipo pamene chiletso chinayamba! Ndiponsotu, chiŵerengero cha omwe anapezeka pa Misonkhano Yachigawo 13 ya “Amithenga a Mtendere Waumulungu” yomwe inachitika m’Malaŵi chinaposa 117,000. Zoonadi, Yehova wadalitsa chikhulupiriro ndi chipiriro chawo.
Chitsanzo cha dalitsoli ndi zomwe zinachitikira mnyamata wotchedwa Machaka. Pamene Machaka anavomereza kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, makolo ake anakhumudwa kwambiri. Iwo anati: “Ngati ufuna kukhala Mboni, uchoke pakhomo pano.” Komabe, izi sizinamufooketse pakuphunzira kwake Baibulo. Pachifukwa chimenecho, makolo ake a Machaka anamlanda zovala zake zonse. Abale anachitapo kanthu mwa kumgulira zovala zina. Pamene makolo ake a Machaka anamva za zimenezi, anamuuza kuti: “Ngati Mboni zizikuthandiza, uchoke pano uzikakhala ndi iwowo.” Atalingalira nkhaniyo mosamalitsa, Machaka anachoka panyumbapo, ndipo banja lina la Mboni mumpingo wa kumaloko, linamtenga ndi kumakhala naye.
Makolo a Machaka ananyansidwa kwambiri kotero kuti anaganiza zochoka kumaloko kuti asakumanenso ndi Mbonizo. Inde izi zinali zovuta kwa Machaka, koma anapeza chitonthozo pamene abale anakambitsirana naye Salmo 27:10, limene limati: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.”
M’kupita kwa nthaŵi makolo a Machaka analeka kutsutsa kwambiri ndipo Machaka anaganiza zobwereranso kunyumba. Mwachionekere kutsimikiza mtima kwa mwana wawo kuti atumikire Yehova kunawakhudza kwambiri chifukwa nawonso anafuna kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova! Anapezekanso pa Msonkhano Wachigawo wa “Amithenga a Mtendere Waumulungu” kwa masiku onse atatu, ndipo anasonkhezereka kulengeza kuti: “Zoonadi ili ndi gulu la Mulungu.”
Zoona, chitsutso chingabweretsedi chiyeso, koma amithenga okhulupirika a Mulungu sabwerera m’mbuyo. Molimba mtima amapitirizabe, podziŵa kuti “chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi [“chiyanjo,” NW].” (Aroma 5:3, 4) Mboni za Yehova m’Malaŵi zingachitiredi umboni kuti chipiriro chimabweretsa dalitso la Mulungu.