“Imeneyi Ndiyo Interlinear ya Chipangano Chatsopano Yabwino Koposa”
NDIMO mmene Dr. Jason BeDuhn anafotokozera za The Kingdom Interlinear Translation of the Greek Scriptures [Baibulo la Kingdom Interlinear la Malemba Achigiriki]. Iye anafotokoza kuti:
“Ndangomaliza kumene kuphunzitsa kosi pa Religious Studies Department of Indiana University [Dipatimenti Yamaphunziro a Zachipembedzo pa Univesite ya Indiana], Bloomington, [U.S.A.] . . . Imeneyi kwenikweni ndi kosi yokhudza mabuku a m’Baibulo a Uthenga Wabwino. Thandizo lanu linali la makope a The Kingdom Interlinear Translation of the Greek Scriptures amene anali kugwiritsiridwa ntchito ndi ophunzira anga monga ena mwa mabuku ophunzirira m’kalasilo. Mabuku ang’onoang’ono ameneŵa anali othandiza kwambiri pakosi imeneyi ndipo ophunzira anga anawakonda kwambiri.”
Kodi nchifukwa chiyani Dr. BeDuhn amagwiritsira ntchito Kingdom Interlinear pamakosi ake a pakoleji? Iye anayankha kuti: “Kunena mwachidule, imeneyi ndiyo interlinear ya Chipangano Chatsopano yabwino koposa imene ilipo. Ndine katswiri wa Baibulo wophunzitsidwa bwino, ndipo ndimadziŵa mabuku ndi ziŵiya zogwiritsira ntchito pophunzitsa maphunziro amakono a Baibulo, komabe, sindine mmodzi wa Mboni za Yehova. Koma buku labwino kwambiri ndimalizindikira ndikaliona, ndipo komiti yanu yotchedwa ‘Komiti Yotembenuza Baibulo la New World’ inachita ntchito yake mwaluso. Katembenuzidwe kanu ka m’Chingelezi ka interlinear nkolongosoka ndiponso sikasinthasintha moti woŵerenga amazindikira bwino kusiyana kwa katchulidwe ka zinthu, mwambo, ndi malingaliro a anthu olankhula Chigiriki ndi mmene ifeyo timachitira. Baibulo lanu la ‘New World Translation’ ndi matembenuzidwe abwino kwambiri, matembenuzidwe otsatira mawu alionse monga momwe alili opanda mafotokozedwe amwambo pofuna kukhala lokhulupirika ku Chigiriki monga momwe amachitira otembenuza ena. Pazifukwa zambiri, Baibulo limeneli nlabwino kwambiri kuposa mabaibulo abwino kwambiri amene akugwiritsiridwa ntchito lerolino.”
Baibulo la The Kingdom Interlinear Translation of the Greek Scriptures limafalitsidwa ndi Mboni za Yehova pofuna kuthandiza anthu okonda Mawu a Mulungu kuti adziŵe bwino zimene zili m’Baibulo lolembedwa m’Chigiriki choyambirira. Kulamanzere la Baibulo la Kingdom Interlinear kuli The New Testament in the Original Greek [Chipangano Chatsopano m’Chigiriki Choyambirira] (lolembedwa ndi B. F. Westcott ndi F. J. A. Hort). Mawu a m’Chingelezi otembenuzidwa monga momwe alili akupezeka pansi pa Mawu a m’Chigiriki. M’danga laling’ono limene lili kulamanja patsamba lililonse la Kingdom Interlinear muli mawu a m’Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures, zimene zimakupatsani mwaŵi wosiyanitsa pakati pa matembenuzidwe a mu interlinear ndi mmene Baibulolo linatembenuzidwira m’Chingelezi chamakono.