Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 3/1 tsamba 32
  • Msonkhano “Wachilendo” Utamandidwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Msonkhano “Wachilendo” Utamandidwa
  • Nsanja ya Olonda—1998
Nsanja ya Olonda—1998
w98 3/1 tsamba 32

Msonkhano “Wachilendo” Utamandidwa

MUULUTSI wina wa ku Lima, Peru, anali kuzikayikira kwambiri Mboni za Yehova. Komabe, atapezeka pa umodzi wa misonkhano yawo yachigawo, maganizo ake anasinthiratu. Kwenikweni, anachita chidwi kwambiri kotero kuti anayamikira Mboni za Yehova pamaso pa omvetsera ake a pa wailesi. Zotsatirazi ndizo zina mwa zimene ananena:

“Msonkhanowo unali wachilendo zedi. Pansi panalibe pepala lililonse kapena wamalonda aliyense pafupi. Magalimoto anali kuyenda bwino lomwe mosatsekerezana. Anthu 5,200 anapita modzifunira ku bwalo lamaseŵero, ndipo aliyense anatenga ndowa yake, kansalu kake, chopukutira fumbi, chowolera zinyalala, tsache, bulasho, magolovesi, ndi sopo wake wotsukira ndi kukwechesa malowo. Pomwe panafunikira kupaka utoto, anapakapo utoto. Ndipo ndani anapereka ndalama zochitira zimenezo? Iwo eniwo ndiwo anapereka! Akauzidwa za chinachake chimene chifunikira kuchitidwa, onse amapereka ndalama za m’thumba mwawo. Kunena zoona, Tchalitchi cha Katolika chili mtulo pankhani zimenezi. Ndikufuna kuthokoza Mboni za Yehova ndi oyang’anira chochitika chimenechi. Ndipo ndikuwauza kuchokera pansi pa mtima wanga kuti, Mulungu akuthandizeni ndi kukudalitsani.”

M’mizinda ya padziko lonse lapansi chaka chino, Mboni za Yehova zidzakhala ndi Msonkhano Wachigawo wa “Njira ya Moyo ya Mulungu.” Kodi mudzapezekako?

[Mawu Otsindika patsamba 32]

“Pansi panalibe pepala lililonse”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena