“Zamphamvu Ndiponso Zokhutiritsa”
“KUYAMBIRA maŵa, ndidzaligwiritsira ntchito polalikira, chifukwa chakuti mfundo zimene lili nazo ndi zamphamvudi ndiponso zokhutiritsa,” analemba motero mmodzi wa Mboni za Yehova ku France. Mboni ina ku United States inalemba kuti: “Ndinaliŵerenga nthaŵi yomweyo ndipo ndidzaligwiritsira ntchito mu utumiki wakumunda mosazengereza, popeza kuti tikukumana ndi anthu ochuluka amphwayi ndiponso amene sakhulupirira Baibulo.” Kodi anali kunena za chiyani? Za brosha lamasamba 32 lamutu wakuti Buku la Anthu Onse, limene linatulutsidwa ndi Watch Tower Society pa Misonkhano Yachigawo ya “Kukhulupirira Mawu a Mulungu” imene inachitika mu 1997/98.
Chofalitsa chimenechi chinakonzedwera anthu ena—awo amene angakhale ophunzira koma amene sakudziŵa zambiri ponena za Baibulo. Anthu ochuluka ameneŵa ali ndi malingaliro ena ponena za Baibulo, ngakhale kuti iwo sanaliŵerengepo. Chifuno cha broshali ndicho kukhutiritsa woŵerenga kuti Baibulo nloyenera ngakhale kungolifufuza kokha. Broshali silikakamiza woŵerenga kuti avomereze lingaliro lakuti Baibulo nlouziridwa ndi Mulungu. M’malo mwake, limalola choonadi kudzilankhulira chokha. Mawu ake sasonyeza kudzitukumula koma ndi osavuta kumva ndiponso olunjika.
Monga momwe ndemanga zogwidwa mawu pamwambapo zikusonyezera, amene analipo pamisonkhanoyi anali ofunitsitsa kugwiritsira ntchito brosha limeneli mu utumiki wawo wakumunda. Mwachitsanzo, ku France analinganiza ndawala yapadera ya kuchitira umboni pa August 23 ndi 24 pamene alendo achinyamata zikwi mazana ambiri ochokera padziko lonse lapansi anakumana ku Paris kaamba ka Tsiku Ladziko Lonse la Achinyamata. Mboni ngati 2,500 (makamaka a zaka zakubadwa zapakati pa 16 ndi 30) anagaŵira makope 18,000 a broshali a m’Chifrenchi, Chijeremani, Chingelezi, Chipolishi, Chispaniya, ndi Chitaliyana.
Tiyeni tiyesetse kugwiritsira ntchito broshali, Buku la Anthu Onse, mu utumiki wathu. Chofalitsa chimenechi chikhaletu chothandiza kwambiri pokhutiritsa anthu a mitima yabwino kuti ayenera kudzifufuzira okha Baibulo.