Dzakhale Nafeni Pachochitika Chapadera Loŵeruka, April 11, 1998
MBONI ZA YEHOVA zikukupemphani kuti mudzakhale nazo pokumbukira mphatso ya Mulungu ya Mwana wake, Yesu Kristu. Mphatso imeneyi inapatsa anthu chiyembekezo cha kukhala ndi moyo wosatha padziko lapansi.—Yohane 3:16.
Chaka chino Chikumbutso cha imfa ya Yesu chidzakhalapo Loŵeruka, April 11, dzuŵa litaloŵa. Tsiku limenelo likulingana ndi tsiku la Nisani 14 la pakalenda ya m’Baibulo yotsatira kayendedwe ka mwezi. Chonde funsani Mboni za Yehova za kwanuko kuti zikuuzeni malo ndi nthaŵi yake.