Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 7/15 tsamba 32
  • “Chitsanzo cha Umodzi ndi Ubale”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Chitsanzo cha Umodzi ndi Ubale”
  • Nsanja ya Olonda—1998
Nsanja ya Olonda—1998
w98 7/15 tsamba 32

“Chitsanzo cha Umodzi ndi Ubale”

Ndimo mmene mkazi wina anafotokozera zimene Mboni za Yehova zinachita iye atapsinjika mtima ndi kumwalira kwa mmodzi wa a m’banja mwake. Iye anati:

“Moimira banja langa ndi ine yemwe, ndikufuna kuthokoza Mboni za mumpingo wachitaliyana ku Freiburg, Germany. Kusiyapo mbale wanga Antonio ndi mkazi wake, Anna, a m’banja langa si Mboni za Yehova. Kwa nthaŵi yaitali takhala tikutsutsa za chipembedzo chimene anasankha, ngakhale kuti nthaŵi zonse timachilemekeza.

“Koma tsopano, tiyenera kusintha malingaliro. Kwenikweni, taona chitsanzo cha ubale ndi chikondi chimene sitikanachiyembekezera nkomwe.

“Mwachisoni, Anna anamwalira mwadzidzidzi pangozi yagalimoto. Popeza kuti timakhala ku Italy, sitinathe kupereka chitonthozo chachikulu kwa mbale wanga Antonio ndi kwa ana ake. Koma abale ake a Mboni amthandiza. Amthandiza mwa kukhalapo kwawo, mawu awo, chikhulupiriro chawo, chichirikizo chawo chakuthupi, cha m’maganizo, ndi chandalama. Popeza kuti sindingathokoze mpingowo pandekha, ndikufuna kuwathokoza kudzera mwa magazini yanu chifukwa cha chitsanzo chawo cha umodzi ndi ubale chimene sitidzaiŵala.”

Tikuyamikira ndemanga zokoma mtima za mkaziyu. Monga momwe anaonera, Mboni za Yehova zili gulu la padziko lonse la abale. (1 Petro 2:17) Iwo amakulitsa chikondi cholimba pakati pawo, podziŵa kuti chikondi “ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.” (Akolose 3:14) Ngakhale pamikhalidwe yomvetsa chisoni kwambiri, imene ingatigwere tonsefe, Mboni za Yehova zimamamatira kwa Mulungu ndi kwa anthu ake.​—Miyambo 18:24; Mlaliki 9:11; Yohane 13:34, 35.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena