Nkhondo Yomwe Inawononga Zaka za Zana la 19
1914
POKUMBUKIRA za zaka chikwi zatsopano, Charley Reese, wolemba nyuzipepala ya The Orlando Sentinel, analemba kuti: “Nkhondo ya mu 1914-18 yomwe inawononga zaka za zana la 19 sinathebe.” Kodi iye anatanthauzanji? Iye anafotokoza kuti: “Mbiri sigonera. Zaka za zana la 19—zofotokozedwa mwa zikhulupiriro zake, zitsimikizo, malingaliro ndi makhalidwe abwino—sizinathe pa Jan. 1, 1901. Zinatha mu 1914. Nthaŵi imeneyo mpamenenso zaka za zana la 20 zinayamba, zofotokozedwanso mofananamo. . . .
“Mwachionekere, mikangano yonse imene yachitika ife tilipo ndi moyo inachokera kunkhondo imeneyo. Pafupifupi zonse za maphunziro ndi zikhalidwe zimene takhala nazo zinayambika ndi nkhondo imeneyo. . . .
“Ndiganiza kuti nkhondoyo inasokoneza zinthu chifukwa chakuti inathetsa chikhulupiriro chimene anthu anali nacho chakuti iwo angalamulire zimene zidzawachitikira mtsogolo. . . . Nkhondoyo inachititsa anthu kukana chikhulupiriro chimenecho. Palibe gulu lililonse mwa magulu omenyanawo limene linaganizapo kuti zidzakhala mmene zinakhalira. Inawononga ufumu wa Britain ndi ufumu wa France. Inapha anthu ofunika kwambiri a mbadwowo ku Britain, France ndi Germany. . . . M’nthaŵi yochepa chabe, inapha anthu 11 miliyoni.”
Kwazaka zoposa 120, Mboni za Yehova zakhala zikufotokoza kuti 1914 inali mapeto a zimene Yesu anazitcha “nthaŵi zawo za anthu akunja.” (Luka 21:24) M’chaka chimenecho, Yesu Kristu woukitsidwa ndi wokwezekayo anaikidwa monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba. Mwa Ufumu umenewo, Yehova Mulungu adzachotseratu mavuto onse omwe akhala akuchitika m’zaka za zana lino.—Salmo 37:10, 11; Mlaliki 8:9; Chivumbulutso 21:3, 4.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Chithunzi cha U.S. National Archives