“Akatolikafe Tili ndi Zambiri Zoti Tiphunzire kwa Iwo”
MAWU ameneŵa onena za Mboni za Yehova ananenedwa ndi mphunzitsi ku Bari, Italy, panthaŵi yake yophunzitsa kalasi za mbiri ya chipembedzo pasukulu yasekondale. Mphunzitsi anali atauza kalasilo kuti adzigwiritsira ntchito makaseti a vidiyo monga zothandizira kuphunzira. Atamva zimenezi, mmodzi wa ophunzirawo, Roberto wazaka 18, anapempha mphunzitsiyo kuphatikizapo chipembedzo chake m’makambitsiranowo. Anapereka kaseti ya vidiyo kwa mphunzitsiyo yakuti Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name. Mphunzitsiyo analandira mphatso ya Robertoyo, ndipo kalasi lonse la ophunzira pafupifupi 30 anaonera. “Onse anachita chidwi ndi mgwirizano, dongosolo, ndiponso chikondi chimene chili pakati pa Mboni za Yehovazo,” akutero Roberto. “Anadabwanso kwambiri pomva kuti magazini 40 miliyoni a Nsanja ya Olonda ndi magazini 36 miliyoni a Galamukani! amasindikizidwa mwezi uliwonse.”
“Sindimadziŵa kuti mumachita zinthu mwadongosolo chonchi,” anatero ophunzira anzake a Roberto atatha kuonera vidiyoyo. Kunena za Mboni za Yehova, mphunzitsiyo anauza kalasilo kuti: “Onani mmene chikhulupiriro chawo chimawasonkhezera kukhala ogwirizana ndiponso adongosolo. Akatolikafe tili ndi zambiri zoti tiphunzire kwa iwo.” Vidiyoyi ndi makambitsirano a m’kalasimo amene anatsatirapo anathandiza kudziŵa bwino Mboni za Yehova.