Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 2/1 tsamba 8
  • Kufunafuna Mulungu Woona Kufupidwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufunafuna Mulungu Woona Kufupidwa
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Baibulo la Berleburg
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kulimbana ndi Zilombo Ziwiri Zoopsa
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Zimene Zili M’buku la Chivumbulutso Zimakhudzanso Adani a Mulungu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Yehova Waulula “Zimene Ziyenera Kuchitika Posachedwapa”
    Nsanja ya Olonda—2012
Nsanja ya Olonda—1999
w99 2/1 tsamba 8

Olengeza Ufumu Akusimba

Kufunafuna Mulungu Woona Kufupidwa

M’ZAKA za zana lakhumi B.C.E., ufumu wamafuko aŵiriwo wa Yuda unadzazidwa ndi kulambira konyenga. Komabe, kulambira mafano kwakukulu kumeneku kuli mkati, kunali munthu amene mtima wake unali wabwino kwa Mulungu. Dzina lake anali Yehosafati. Mneneri Yehu anati ponena za iye: “Zapezeka zokoma mwa inu, popeza . . . mwalunjikitsanso mtima wanu kufuna Mulungu.” (2 Mbiri 19:3) Mofananamo lerolino, mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zimenezi, anthu mamiliyoni ‘alunjikitsa mitima yawo’ kufunafuna Mulungu woona, Yehova. (2 Timoteo 3:1-5) Zimenezo zikusonyezedwa ndi nkhani iyi yochokera ku Togo, ku West Africa.

Casimir ankaphunzira kusukulu ya Akatolika ndipo anachita nawo mwambo wa Misa koyamba ali ndi zaka zisanu ndi zinayi. Komabe, pamene anakwanitsa zaka 14, Casimir anali atasiya kupita ku tchalitchi. Zimenezi zinamuchititsa mantha chifukwa anali kuganiza kuti kusapezeka kwake pa Misa kudzam’pititsa ku helo wamoto, kapena ngakhalebe ku purigatoriyo.

Kusukulu, Casimir analoŵa nawo m’kagulu ka achinyamata amene ankakumana kamodzi pamlungu ndi kumaphunzira Baibulo. Ndiponso anayamba kuŵerenga Baibulo payekha. Panthaŵi ina Casimir anaŵerenga m’buku la Chivumbulutso za chilombo chochititsa mantha chimene chinatuluka m’nyanja. (Chivumbulutso 13:1, 2) Pamene anafunsa mtsogoleri wa kagulu ka ophunzira Baibuloko za icho, anauzidwa kuti chilombocho chinali chenicheni ndi kuti chidzatulukadi m’nyanja. Yankho limeneli linamuopsa Casimir chifukwa sanali kukhala kutali ndi m’mphepete mwa nyanja ya Atlantic. Sadakayikire kuti adzakhala mmodzi wa anthu oyamba kugwidwa ndi chilombocho.

Casimir anayamba kusunga ndalama zake kuti athaŵire kuchipululu cha kumpoto kuti azembe chilombocho. Anauza mnzake wa m’kalasi za maganizo ake. Pokhala wa Mboni za Yehova, mnzakeyo anam’tsimikizira kuti palibe chilombo chenicheni chimene chidzatuluke m’nyanja. Posakhalitsa, Casimir anaitanidwa ku misonkhano ku Nyumba ya Ufumu. Anakondwera nayo misonkhanoyo ndipo anayamba kupezekapo mokhazikika. Anavomeranso kuti adziphunzitsidwa Baibulo panyumba.

Pamene Casimir anali kupitiriza kuphunzira, abale ake anayamba kumuletsa. M’banja mwawo ankalambira makolo ndipo ankadya nyama yosakhetsa magazi yotsala atatha kupereka nsembe. Pamene mwaulemu Casimir anakana kudya nyamayo, anaopsezedwa ndi kuuzidwa kuti achoke panyumbapo. Casimir sanatekeseke, ndipo sanam’vutitse n’komwe. Komabe, kwa miyezi itatu nyama yokha yotere ndi yomwe inkakonzedwa pa chakudya cha banjalo. Casimir anali kuvutika kuti apeze chakudya chokwanira, koma anapirira zimenezi ndiponso mavuto ena.

Casimir anapitiriza kukula mwauzimu kufikira pa kudzipatulira ndi ubatizo. Pambuyo pake anaikidwa kukhala mtumiki wotumikira ndipo anali nawo m’kalasi yachinayi ya Sukulu Yophunzitsa Utumiki ku Togo. Pakali pano, akusangalala ndi ntchito yodzifunira yomwe akuchita panthambi.

Inde, mawu a Davide akhala oona nthaŵi zambiri akuti: “Ukamfunafuna [Yehova] iye udzampeza.”​—1 Mbiri 28:9.

[Zithunzi patsamba 8]

Casimir (kulamanja) akusangalala ndi ntchito yodzifunira panthambi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena