Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 2/1 tsamba 24
  • Chisumbu Chakutali Komanso Chaching’ono

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chisumbu Chakutali Komanso Chaching’ono
  • Nsanja ya Olonda—1999
Nsanja ya Olonda—1999
w99 2/1 tsamba 24

Chisumbu Chakutali Komanso Chaching’ono

AFOTOKOZI omwe amatchulidwa kaŵirikaŵiri onena zachisumbu cha St. Helena ndi “chakutali” komanso “chaching’ono.” Afotokozi ameneŵa n’ngoyenera chisumbuchi, chifukwa utali wake ndi wokwana makilomita 17 ndipo ufupi wake ndi wokwana makilomita 10. Ndipo pali mtunda wa makilomita 1,950, kuchokera kudera loyandikana nalo la kumwera chakumadzulo kwa gombe la Afirika. N’kuno komwe Napoléon Bonaparte anatumizidwa kudzakhala monga kapolo mu October 1815 mpaka pamene anamwalira mu May 1821.

Panyanja chisumbuchi chimaoneka ngati linga lalikulu. Koma kwenikweni ndi volokano imene inasiya kuphulika ya m’nyanja ya Atlantic yokhala ndi therezi lotsetsereka lautali wokwana mamita 500 mpaka 700. Pakati pa chisumbuchi, pali phiri lalitali kwambiri la Actaeon, lautali wokwana mamita 818. Chifukwa cha mphepo yozizira yochokera kumwera kwa nyanja ya Atlantic ndi kayendedwe ka madzi, chisumbuchi chili ndi mphepo yozizira bwino kwambiri. Kuchokera ku gombe kumapita cha kumapiri, pali nyengo ndi zomera zosiyanasiyana.

Chisumbu cha St. Helena chinakhala cha Abritishi kuyambira chakumapeto kwa zaka za zana la 17. Pachisumbuchi pali Azungu, Amwenye ndi anthu Akuda, amene amapanga chiŵerengero chokwanira pafupifupi 5,000. Onse amalankhula Chingelezi, koma chomveka mosiyana. Pachisumbuchi palibe ndi bwalo la ndege lomwe; njira yokha yopitira ku mayiko akunja ndi kuyenda pasitima yapamadzi basi, kudzera ku South Africa ndi England. Ndiponso, mawailesi akanema anayamba kupezeka cha m’ma 1990, ndi chithandizo cha masetilaiti.

Kumayambiriro kwa ma 1930, uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kwanthaŵi yoyamba unafika pamagombeŵa. (Mateyu 24:14) Kwa zaka zonsezi, apachisumbuchi apeza chuma chimenechi chofunika koposa katundu wa kuthupi. (Mateyu 6:19, 20) Lerolino, Mboni iliyonse ku St. Helena ili ndi anthu 31 yoti iwalalikire, chiŵerengero chabwino koposa padziko lonse!

[Mapu patsamba 24]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

St. Helena

JAMESTOWN

Levelwood

AFIRIKA

NYANJA YA ATLANTIC

St. Helena

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena