Kodi Mukuganiza za Ukwati?
Ngati tingayerekeze vuto la kusudzulana padziko lonse ndi chivomezi, ndiye kuti dziko la United States lili ngati pachimake. Chaka china posachedwa pompa, maukwati oposa miliyoni imodzi anatha kumeneko—maukwati aŵiri mphindi imodzi iliyonse. Koma muyenera kuti mukudziŵa kuti dziko la United States si lokhalo lomwe lili ndi mavuto a ukwati.
MALINGA ndi kafukufuku wina, ziŵerengero za zisudzulo ku Canada, England ndi Wales, France, Greece, ndi Netherlands zaŵirikiza kuposa kaŵiri chiyambire 1970.
Tili ndi chifukwa chokhulupirira kuti ambiri amakwatirana chifukwa amakondana ndipo amafuna kukhala limodzi moyo wawo wonse. Koma chisoni chake n’chakuti nthaŵi zambiri zolinga zawo zakuti akhale ndi ukwati wachimwemwe sizikwaniritsidwa ayi—zimangokhala ngati maloto. Atadziŵa zenizeni, ambiri anena kuti anafulumira kukwatira kapena kuti sanasankhe bwino mnzawo kapena zonse ziŵiri.
N’chifukwa chiyani maukwati ambiri amalephereka? “Chifukwa chachikulu ndicho kusakonzekera,” akutero wolemba buku lonena za kupalana ubwenzi. Akuwonjeza kuti: “Poyesa kuthandiza mabanja omwe ali m’mavuto, zinthu ziŵiri zimachitika—ndimamva chifundo ndi mkwiyo. Ndimawamvera chifundo chifukwa sanapeze zolinga zawo zokhala ndi unansi wokhutiritsana. Ndimakwiya chifukwa iwo sadziŵa mmene ntchitoyo imavutira.”
Inde, ambiri amakwatira akudziŵa zochepa zofunika kuti ukwati ukhale wabwino kapena asakudziŵa kalikonse. Koma zimenezi n’zosadabwitsa ayi. Mphunzitsi wina anati: “Kodi ndi achinyamata angati amene amapita ku koleji kukaphunzira za khalidwe la makoswe ndi la abuluzi, koma osaphunzira za khalidwe la anthu aŵiri otchedwa mwamuna ndi mkazi wake?”
Kodi mukuganiza za ukwati—kaya za ukwati wa m’tsogolo kapena umene mulimo tsopano? Ngati mukutero, zindikirani kuti unansi weniweni n’ngwosiyana kwambiri ndi zimene amaonetsa m’mafilimu, m’mapologalamu a pawailesi yakanema, ndi m’mabuku a nthano za chikondi. Komanso, tingati ukwati wa anthu aŵiri ofikapo amene akukondanadi ndiwo dalitso lochokera kwa Mulungu. (Miyambo 18:22; 19:14) Nangano mungadziŵe bwanji kuti ndinu wokonzeka kuchita zimene ukwati umafuna? Kodi muyenera kupenda mfundo zotani posankha mnzanu? Komanso ngati ndinu wokwatira, kodi mungachite zotani kuti mupeze chimwemwe chokhalitsa mu ukwati wanu?