Akuluakulu a Boma Ayamikira Mboni
KU Cádiz, ku Spain, kudoko lopezeka pamtunda wa makilomita 500 kumwera chakumadzulo kwa Madrid, woyang’anira mzinda Doña Teófila Martínez anapereka kwa Mboni za Yehova chikwangwani chaulemu (chomwe chili pamwambachi). Mawu ake akuti: “Bungwe loyang’anira mzinda wa Cádiz kwa Mboni za Yehova poyamikira kugwirizana kwawo ndi ntchito yomwe agwira m’malo mwa anthu a mumzindawu.” Kodi Mbonizo zinachita chiyani kuti zilandire mphatso yaulemu imeneyi?
Inapatsidwa kwa izo poyamikira ntchito imene Mbonizo zinachita yokonza zinthu zina za pabwalo la maseŵero la mumzindawu. Mapeto amilungu ingapo, Mboni zambirimbiri zinadzipereka kuthandiza kukonza m’zimbudzi za pabwalo la maseŵero la Carranza. Tsopano, onse amene amafika pabwalo limeneli amathandizika ndi mipope, mapaipi a madzi, ndiponso pansi pomwe anakonza.
Kwanthaŵi yaitali, Mboni za Yehova zakhala paubwenzi ndi anthu a mumzinda wa Cádiz. Chaka chilichonse, Bungwe loyang’anira mzindawu limalola Mboni kuchita msonkhano wawo wachigawo wapachaka pabwalo lamaseŵero la Carranza. Chotero, Mboni n’zofunitsitsa kuchita zomwe zingathe pothandiza kusunga bwalo la maseŵero limeneli lili labwino.
Komabe, kuphatikiza pantchito yakuthupi yochitika mwa apo ndi apo imeneyi, Mboni za Yehova nthaŵi zonse zimapita kumalo oyandikana ndi mzindawu kukathandiza anthu mwanjira ina. Zimalengeza “uthenga wabwino” wa Ufumu wa Mulungu. Koma, sizichita utumiki wawo poyera ndi cholinga choti anthu awayamikire. Zimachita momvera lamulo la Yesu lolalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu’ ndi ‘kuphunzitsa anthu amitundu yonse.’ (Mateyu 24:14; 28:19) Mwanjira imeneyi, Mboni za Yehova zimathandiza anthu a mumzindawu mwa kuwaphunzitsa kuyenda “m’khwalala la chilungamo.”—Miyambo 12:28.