Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 4/15 tsamba 30
  • Kodi Mukukumbukira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukukumbukira?
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Muli ndi Mzimu Wosafa?
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Kodi Muli ndi Mzimu Wosafa?
    Kodi Muli ndi Mzimu Wosafa?
  • Lino Ndilo Tsiku la Chipulumutso!
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Kodi Yesu Amapulumutsa Motani?
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 4/15 tsamba 30

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwasangalala kuŵerenga makope aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Chabwino, yesani kuyankha mafunso otsatirawa:

◻ Kodi n’chifukwa chiyani mawu a Paulo akuti “akazembe m’malo mwa Kristu” ali oyenerera pofotokoza Akristu odzozedwa? (2 Akorinto 5:20, NW)

Kale, akazembe ankatumizidwa kwenikweni panthaŵi yachidani kuti akakambirane ndi adani awo pofuna kupeŵa nkhondo. (Luka 14:31, 32) Ndiye poti anthu ochimwa ali otalikirana ndi Mulungu, watumiza akazembe ake odzozedwa kuti auze anthu mfundo za mmene anthuwo angayanjanirane ndi Mulungu, kuwalimbikitsa kuyesetsa kukhala pamtendere ndi Mulungu.​—12/15, tsamba 18.

◻ Kodi ndi zinthu zinayi ziti zimene zinalimbitsa chikhulupiriro cha Abrahamu?

Choyamba, anasonyeza chikhulupiriro chake mwa Yehova mwa kumvera Mulungu akalankhula (Ahebri 11:8); chachiŵiri, chikhulupiriro chake chinali chogwirizana kwambiri ndi chiyembekezo chake (Aroma 4:18); chachitatu, Abrahamu anali kuyankhula ndi Mulungu kaŵirikaŵiri; ndipo chachinayi, Yehova anachirikiza Abrahamu pamene anatsatira chitsogozo cha Mulungu. Zinthu zofananazo zingalimbitse chikhulupiriro chathu lerolino.​—1/1, masamba 17, 18.

◻ Kodi mawu akuti “Musatitengere kokatiyesa” amatanthauzanji? (Mateyu 6:13)

Timapempha Mulungu kuti asatilole kulephera pamene tiyesedwa kusamvera iye. Yehova angatitsogoze kuti tisagonje pamene tiyesedwa ndi Satana, “woipayo.” (1 Akorinto 10:13)​—1/15, tsamba 14.

◻ Kodi munthu ayenera kuchitanji kuti akhululukidwe ndi Mulungu pa cholakwa chake?

Poulula machimo kwa Mulungu tiyenera kukhalanso achisoni ndi kusonyeza “zipatso zakuyenera kulapa mtima.” (Luka 3:8) Mzimu wolapa ndi kufunitsitsa kukonza cholakwacho zidzatisonkhezeranso kupempha thandizo lauzimu kwa akulu achikristu. (Yakobo 5:13-15)​—1/15, tsamba 19.

◻ Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kukhala odzichepetsa?

Munthu wodzichepetsa ndi woleza mtima ndi wosakwiya msanga, ndipo sadziona kukhala munthu wofunika kwambiri. Kudzichepetsa kumadzetsa mabwenzi oona amene amakukondani. Chofunika kwambiri, kumadzetsa madalitso a Yehova. (Miyambo 22:4)​—2/1, tsamba 7.

◻ Kodi pali kusiyana kwakukulu kotani pakati pa imfa ya Yesu ndi imfa ya Adamu?

Adamu anayenera kufa, chifukwa modzifunira sanamvere Mlengi wake. (Genesis 2:16, 17) Koma Yesu sanayenere kufa mpang’ono pomwe, popeza kuti “sanachita tchimo.” (1 Petro 2:22) Choncho pamene Yesu anafa, iye anali ndi chinachake cha mtengo waukulu kwambiri chimene Adamu wochimwayo analibe pa imfa yake​—ufulu wokhala ndi moyo wangwiro waumunthu. Choncho, imfa ya Yesu inali nsembe yoombola mtundu wa anthu.​—2/15, masamba 15, 16.

◻ M’masomphenya aulosi a Ezekieli, kodi mzinda unaimira chiyani?

Pakuti mzindawo uli pakati pa dziko wamba (losapatulika), uyenera kukhala chinthu cha padziko lapansi. Choncho ukuoneka kuti ukuimira uyang’aniro wa padziko lapansi umene udzapindulitsa onse olungama amene adzakhala padziko lapansi.​—3/1, tsamba 18.

◻ Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anasambitsa mapazi a ophunzira ake pochita Paskha mu 33 C.E.?

Yesu sanali kuyambitsa mwambo wosambitsa mapazi. M’malo mwake, anali kuthandiza atumwi ake kusintha maganizo awo​—kuti akhale odzichepetsa ndi ofunitsitsa kuchita ntchito zonyozeka m’malo mwa abale awo.​—3/1, tsamba 30.

◻ Pamene tikuphunzitsa ena, kodi n’chiyani chofunika kwambiri kuposa maluso achibadwa?

Ndi mikhalidwe imene tili nayo ndi zizoloŵezi zauzimu zimene takulitsa zimene ophunzira angatsanzire. (Luka 6:40; 2 Petro 3:11)​—3/15, masamba 11, 12.

◻ Kodi okamba nkhani poyera angawongolere motani kuŵerenga kwawo Malemba?

Mwa kukonzekera. Inde, mwa kuŵerenga mokweza mobwerezabwereza mpaka atayamba kuŵerenga mosaphonyaphonya. Ngati pali makaseti a Baibulo, n’kwanzeru kumamvetsera mmene woŵerengayo akugogomezera ganizo ndi kusinthasintha mawu ndi kumvetseranso mmene mayina ndi mawu achilendo amatchulidwira.​—3/15, tsamba 20.

◻ Kodi ‘mzimu umabwerera kwa Mulungu’ motani munthu akafa? (Mlaliki 12:7)

Popeza kuti mzimu ndiwo mphamvu ya moyo, ‘umabwerera kwa Mulungu’ m’lingaliro lakuti chiyembekezo chilichonse cha moyo wam’tsogolo ponena za munthuyo chimatsala m’manja mwa Mulungu basi. Mulungu yekha ndiye angabwezeretse mzimuwo, kapena mphamvu ya moyo, kubwezeretsa munthuyo ku moyo. (Salmo 104:30)​—4/1, tsamba 17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena