Chiwawa—Chidzatheratu Posachedwapa!
“Dziko Lifika Poopsa Chifukwa cha Chiwawa”—The New York Times, United States.
“Chiwawa pa Nyumba”—O Globo, Brazil.
“Chiwawa Chitsata Akazi Padziko”—The Globe and Mail, Canada.
MITU ya nkhani imeneyi yotengedwa m’nyuzipepala za ku North ndi South America ikuonetsa mkhalidwe wodetsa nkhaŵa umene uli padziko lonse lapansi. Malinga ndi kunena kwa bungwe la zaumoyo la World Health Organization, “chiwawa chamtundu uliwonse chawonjezeka kwambiri pazaka makumi angapo zapitazo.”
Talingalirani maumboni ena odetsa nkhaŵa:
Kuphana. Kumayiko a Latin America ndi Caribbean, anthu pafupifupi 1,250 amafa imfa yochita kuphedwa tsiku lililonse. Chifukwa cha zimenezo, “theka la mayiko a m’chigawocho ali ndi imfa zambiri za achinyamata azaka 15-24 zimene zikuchitika chifukwa cha kuphana.”
Chiwawa kwa ana. Vuto lochitira ana nkhanza mwa kuwamenya, kuwagona, ndi kuwanyoza lili kulikonse kuzungulira dziko lapansi. Mwachitsanzo, “atafufuzafufuza kwa achikulire m’mayiko angapo otukuka anapeza kuti 10%-15% ya ana amagonedwa—makamaka ana aakazi.”
Chiwawa kwa akazi. Atafufuza za kupondereza ufulu wachibadwidwe kochitidwa padziko lonse mu 1997, ofufuza anafika ponena kuti “chiwawa m’banja n’chimene chachititsa akazi ambiri kuvulala pafupifupi m’dziko lililonse padziko lapansi.” (Human Rights Watch World Report 1998) Popeza kuti vuto la chiwawa m’banja n’lofala koma losachitidwa lipoti mofunikira, tsopano likutchedwa “vuto lachinsinsi la m’zaka za zana la 20.”—The Globe and Mail, Canada.
Mofananamo dziko “linadzala ndi chiwawa” masiku a Nowa. (Genesis 6:9-12) Koma Yehova Mulungu anapulumutsa “mlaliki wa chilungamo” ameneyo ndi banja lake “pakulitengera dziko la osapembedza chigumula.” Mulungu adzachita zofananazo m’tsiku lathu. Adzasunga “opembedza” pochotsa achiwawa ndi oipa ndi kusandutsa dziko lapansili paradaiso m’dziko lake latsopano lolonjezedwalo. (2 Petro 2:4-9; 3:11-13) Kodi simukusangalala kudziŵa kuti chiwawa chidzatheratu posachedwapa?