Nzeru ‘Yooneratu Zimene Zidzachitika’
“IWO ndi anthu amene ataya nzeru yabwino ndipo alibe kuzindikira. Akanakhala ndi nzeru, akanazindikira ichi ndi kuoneratu zimene zidzachitika kwa iwo.”—Deuteronomo 32:28, 29, Beck.
Mawu amenewa analankhulidwa ndi Mose kwa Aisrayeli pamene iwo anaima m’malire a Dziko Lolonjezedwa. Mose anali kulosera za nthaŵi imene iwo ati adzakane Yehova koma osalingalira konse za zotsatira za kachitidwe kawo kameneko. Mkati mwa zaka mazana angapo zotsatira, Aisrayeli—kuphatikizapo mafumu awo ambiri—ananyalanyaza machenjezo a Mulungu.
Mwachitsanzo, Solomo ankadziŵa lamulo la Mulungu lakuti asamakwatire akazi amene ankalambira milungu ina kusiyapo Yehova. (Deuteronomo 7:1-4) Komabe, iye anakwatira “akazi ambiri achilendo.” Zotsatirapo zake? Mbiri ya m’Baibulo imati: “Kunali, atakalamba Solomo, akazi ake anapambutsa mtima wake atsate milungu ina; ndipo mtima wake sunakhala wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide atate wake.” (1 Mafumu 11:1, 4) Ngakhale anali munthu wanzeru, Solomo analibe nzeru yabwino ‘yooneratu zimene zikachitika’ iye atapanda kumvera lamulo la Mulungu.
Bwanji nanga ponena za ife? Tingapewe zoŵaŵa zambiri ngati tiyamba taganiza mokwana tisanasankhe chochita m’moyo. Mwachitsanzo, Akristu akuchenjezedwa ‘kudzikonzera okha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu.’ (2 Akorinto 7:1) Zimenezi n’zanzeru, komabe ambiri alibe nzeru yabwino yooneratu zimene zingaŵachitikire ngati iwo anyalanyaza uphungu wa Paulo umenewu. Mwachitsanzo, achinyamata ambiri amadetsa matupi awo mwa kusuta fodya akumaganiza kuti kuteroko kumawachititsa kukhala otsogola kwambiri komanso kukhala achikulire. Mmene zimakhalira zachisoni pambuyo pake m’moyo, pamene ambiri amadzadwala matenda a mtima, kansa ya m’mapapu, kapenanso matenda ena a m’mapapu otchedwa emphysema chifukwa cha kusuta!
N’kofunika kuti tiziganiza mozama pa zotsatira zake za zinthu zimene timasankha komanso zochita zathu. Choncho Paulo anali ndi chifukwa chabwino pamene analemba kuti: “Chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.”—Agalatiya 6:7, 8.