Chitsogozo pa Kusankha Mabwenzi Abwino
ACHINYAMATA amafunsa mabwenzi awo m’malo mofunsa makolo kuti awathandize kusankha zovala ndi nyimbo, linatero lipoti la mu Reader’s Digest. Choncho n’kofunika kuti makolo adziŵe mabwenzi a ana awo komanso kumene amaseŵerera.
“Ndi udindo wanu kufufuza,” akutero Esmé van Rensburg, mphunzitsi wamkulu mu dipatimenti ya maphunziro a zamaganizo ndi khalidwe la anthu payunivesite ya ku South Africa. Akuwonjezera kuti: “Inde, ana anu angakukwiyireni, koma sadzapitiriza kukwiya.” Ndiyeno akupereka malangizo otsatiraŵa kwa makolo. Malamulo ayenera kukhala omveka komanso zifukwa zake zikhale zomveka; mvetserani kwa mwanayo; musakwiye, fatsani, ndipo pendani zomwe muti mulankhule. Ngati mwanayo ali kale ndi bwenzi losayenera, kambiranani kwambiri mikhalidwe yoipa imene ubwenziwo wayambitsa m’malo mongoletsa mwanayo kucheza ndi mnzakeyo.
Malangizo abwino kwa makolo akhalapo kwa nthaŵi yaitali m’Mawu a Mulungu, Baibulo. Mwachitsanzo, limati: “Yense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.” (Yakobo 1:19) Malemba amaperekanso langizo labwino ili pa kusankha mabwenzi: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Zitsanzo zimenezi zikusonyeza nzeru imene onse amene amaŵerenga Baibulo ndi chiyamiko ndi kutsatira zimene limanena m’moyo wawo ali nayo.