Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 8/1 tsamba 32
  • Kusankhana Mafuko ndi Chipembedzo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusankhana Mafuko ndi Chipembedzo
  • Nsanja ya Olonda—1999
Nsanja ya Olonda—1999
w99 8/1 tsamba 32

Kusankhana Mafuko ndi Chipembedzo

PAMENE ndinabwera kuno ku United States m’chaka cha 1978, ndinakhulupirira kuti America anathetsa kalekale mavuto ake osankhana fuko, mwakuti panalibe kusiyana pakati pa anthu akuda ndi azungu,” anafotokoza motero Mark Mathabane, wolemba mabuku wa ku South Africa, pamene anafunsidwa ndi a Times magazine. “M’njira zambiri, ndidapeza kuti zidalidi zoona. United States inaoneka kukhala itatsogola kwa zaka zambirimbiri poyerekeza ndi South Africa. Pambuyo pake ndinazindikira ndi mantha aakulu kuti, zambiri sizinasinthebe m’mitima ya anthu.” Kodi ndi chiyani chinam’pangitsa kuti atulukire mkhalidwe wodabwitsa umenewo?

“Nthaŵi imene tsankho loterolo limachitika kwambiri ku America ndi 11 a.m. Lamlungu,” anatero Mathabane. Anaonanso kuti ngakhale m’tchalitchi, anthu samakhala omasuka kulambira limodzi ndi anthu a fuko lina. Ndipo iye anafunsa kuti: “Nanga m’masiku ena a mlungu angamve bwanji?” Kutchula maphunziro kuti ndiwo angathandize kusintha zinthu, Mathabane anati: “Maphunziro amatheketsa munthu kuvomereza kuti anthu ndi amodzi.”

Mboni za Yehova zimavomereza kuti maphunziro ndiwo yankho, koma iwo kwenikweni amaona maphunziro ozikidwa pa Mawu a Mulungu kuti ndiwo angathandize kwenikweni. Inde, Baibulo limaŵathandiza kuphwanya zotchinga za tsankho la mafuko​— ngakhale m’mayiko momwe kudana kwa mafuko kuli kofala. Mlungu uliwonse, m’Nyumba zawo za Ufumu, anthu amafuko ndi mitundu yosiyanasiyana amasonkhana pamodzi kudzaphunzitsidwa malamulo ndi mapulinsipulo a Mawu a Mulungu, Baibulo. Samayendetsa mbale ya zopereka m’misonkhano imeneyi. Muli olandiridwa kudzasonkhana nawo!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena