“Mwamuna Wokondwera ndi Mkazi Wosangalatsa”
KAŴIRIKAŴIRI, anthu ena amadzudzula Mboni za Yehova kuti zimapasula mabanja. Komabe, mabanja ambiri ochita bwino, omwe mmodzi yekha wa okwatiranawo ndiye Mboni ya Yehova, asonyeza kuti zimenezo sizoona m’pang’ono pomwe. Kumvera uphungu wa m’Baibulo m’banja, kumapangitsa banja kukhala lachimwemwe monga momwe kalata yofalitsidwa m’nyuzipepala ya Chifalansa inasonyezera.
“Kwa zaka 28 tsopano, ndakhala mwamuna wokondwera ndi mkazi wosangalatsa amene ndi wa Mboni za Yehova. Analera ana anga asanu, aŵiri mwa iwo anali opeza, koma anawalera ndi kuwasamala mwachikondi osawasiyanitsa ndi enawo. Tsopano monga woyang’anira kampani yomwe ili ndi antchito 45, kunena zoona, nditha kukutsimikizirani kuti ndiye wandithandiza kwambiri kuti ndipambane choncho pantchito yanga. Ichi n’chifukwa chake ndinaganiza zokupatsani umboni woona wa nkhani yomwe inatuluka m’nyuzipepala yomwe ndimakonda kuŵerenga nthaŵi zonse. Nyuzipepalayo inalemba kuti Mboni za Yehova zikupereka chiopsezo kudera lotchedwa Lot-et-Garonne.”
Kalatayo inanenanso kuti: “Sasuta fodya kapena kuledzera. Kodi chimenechi n’chiopsezo? Ali Akristu ololerana omwe samaumiriza munthu wina kutsata malamulo omwe iwo amatsata. Chenicheni n’chakuti ali chitsanzo chabwino m’mbali zambiri. . . . Samawononga chuma kapena kuzembetsa mankhwala ozunguza bongo. Sapanga lumbiro la kusakwatira, ndikukutsimikizirani, iwo amakhala moyo mofanana ndi anthu onse. . . .
“Mwina mungandifunse kuti: Nanga bwanji iweyo suli wa Mboni za Yehova? Chifukwa chake n’chakuti amafuna chikhulupiriro chenicheni chachikristu ndi kudzisunga moona mtima, ndipo ndi ochepa amene amakwanitsa zimenezo.”