Kodi Baibulo Lingatithandize Lerolino?
“PAFUPIFUPI 1 peresenti yokha ya Baibulo lonselija ndiyo yabwino kuiŵerenga, koma kwinako n’kwachabechabe komanso kotha ntchito.” Anatero mnyamata wina. Ambiri angavomerezane naye. Ngakhale kuti Baibulo ndi buku limene likugulitsidwa kwambiri kuposa mabuku ena, anthu mamiliyoni ambiri salilingalira n’komwe ndiponso ziphunzitso zake sazidziŵa.
M’kope lake la m’nyengo ya Khirisimasi ya 1996, nyuzipepala ya ku German yotchedwa Süddeutsche Zeitung inaikira ndemanga kuti “anthu oŵerenga [Baibulo] akucheperachepera. M’nyengo ino ya sayansi ndi kupita patsogolo kwa zinthu zadziko, nkhani za m’Baibulo zikuoneka ngati zachilendo ndi zovuta kuzimvetsa kwa anthu ambiri.” Kufufuza kwachitira umboni lipoti limeneli. Kufufuza kwina kwavumbula kuti ana ambiri sadziŵa kwenikweni kuti kodi Yesu ndani. M’kufufuza kumodzi, ochepera pa theka la anthu amene anafunsidwa anakhoza kufotokoza nkhani za m’Baibulo za mwana woloŵerera ndi Msamariya wachifundo.
Chofalitsa cha Tchalitchi cha Swiss Evangelical chotchedwa Reformiertes Forum chinati chiŵerengero cha anthu ofuna Baibulo mu Switzerland chikusiyana kwambiri ndi mmene chinalili kale. Ngakhalenso omwe ali nalo Baibulo, kaŵirikaŵiri limangotuŵa ndi fumbi m’shelefu. M’Britain namonso zinthu zili chimodzimodzi. Malinga n’kufufuza kwina kumene kunachitika, ngakhale kuti anthu ochuluka ali nalo Baibulo, ambiri a iwo saliŵerenga n’komwe.
Kumbali ina, miyandamiyanda ya anthu padziko lonse, Baibulo amalionera mwina. Amaliona monga Mawu a Mulungu ndipo amalionanso kukhala labwino zedi ndi lopindulitsa. Choncho, amaliŵerenga nthaŵi zonse. Msungwana wina analemba kuti: “Ndimayesa kuŵerenga chaputala chimodzi kapena machaputala aŵiri a Baibulo tsiku lililonse. Limandisangalatsa kwambiri.” Anthu ngati ameneŵa amamvetsetsa zimene Baibulo likuphunzitsa, ndipo amayesa kugwiritsa ntchito uphungu wake m’moyo wawo. Amakhulupirira kuti Baibulo lingaŵathandize m’dziko lino lodzala ndi mavuto.
Nanga inu malingaliro anu n’ngotani? Kodi Baibulo n’lachabechabe m’nthaŵi zamakono zino? Kapena n’labwino zedi ndi lopindulitsa? Kodi Baibulo lingatithandize lerolino?