Chaka Chabwino Kwambiri Kugaŵira Mabaibulo
ANTHU ambiri lerolino kuposa kale, ali ndi Baibulo. Izi n’zimene lipoti la United Bible Societies likunena, popeza mabaibulo amene anagaŵira mu 1998 anaposa amene anagaŵiridwa mu 1997 ndi 500,000. Onse pamodzi, mabaibulo athunthu kapena mbali yake amene anagaŵiridwa padziko lonse anali 585,000,000. “Izi n’zolimbikitsa,” likutero lipotilo. “Lerolino anthu ambiri ali ndi Mawu a Mulungu.”
Ndithudi, pali kusiyana pakati pa kukhala ndi Baibulo ndi kuliŵerenga. Mwachitsanzo, pakufufuza kwina anapeza kuti kuposa 90 peresenti ya nzika za ku United States zili ndi Baibulo, ndipo chiŵerengero chofananacho cha anthu chimakhulupirira kuti m’Baibulo ndimo muli ziphunzitso za makhalidwe abwino. Komabe, 59 peresenti okha n’ngomwe anati amapeza malangizo m’Baibulo. Ndipo 29 peresenti anavomereza kuti “salidziŵa kwenikweni” kapena “salidziŵa n’komwe” Baibulo.
Mboni za Yehova sizimangosindikiza ndi kugaŵira mabaibulo komanso zimapereka kwa anthu maphunziro a Baibulo aulere apanyumba m’mayiko 230. Tsopano mamiliyoni ambiri padziko lonse akupindula ndi pologalamu yophunzitsa Baibulo imeneyi. Akuthandizidwa kugonjetsa mavuto amene amakumana nawo lerolino, ndipo amaphunzira zimene Baibulo limanena pa za m’tsogolo mwabwino mu Ufumu wa Mulungu.—Yesaya 48:17, 18; Mateyu 6:9, 10.
[Zithunzi patsamba 32]
Maphunziro a Baibulo apanyumba (kuyambira pamwamba kumanzere kumka kumanja) Bolivia, Ghana, Sri Lanka, ndi England