Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w00 2/1 tsamba 32
  • Kodi Yehova Adzakukumbukirani Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Yehova Adzakukumbukirani Motani?
  • Nsanja ya Olonda—2000
Nsanja ya Olonda—2000
w00 2/1 tsamba 32

Kodi Yehova Adzakukumbukirani Motani?

“MUNDIKUMBUKIRE, Mulungu wanga.” Kwa maulendo angapo Nehemiya anapempha Mulungu m’mawu amenewo. (Nehemiya 5:19; 13:14, 31) N’kwachibadwa kuti pamene anthu ali m’vuto lalikulu, amatembenukira kwa Mulungu ndi mawu odandaula ngati amenewo.

Koma, kodi anthu amalingalira chiyani pamene akupempha Mulungu kuti awakumbukire? Mwachionekere, iwo amayembekezera Mulungu kuwachitira zoposa kungokumbukira mayina awo. Mosakayikira iwo amayembekezera mofanana ndi momwe anachitira mmodzi wa apandu omwe anaphedwa pamodzi ndi Yesu. Mpandu ameneyu, mosiyana ndi winayo, anachonderera Yesu kuti: “Ndikumbukireni mmene muloŵa Ufumu wanu.” Anafuna kuti Yesu asangomukumbukira chabe kuti iye anali yani koma kum’chitira kanthu kenakake, kumuukitsa.​—Luka 23:42.

Nthaŵi zonse, Baibulo limasonyeza kuti kwa Mulungu, “kukumbukira” kumatanthauza kuchitapo kanthu motsimikiza. Mwachitsanzo, dziko lapansi litamizidwa ndi chigumula kwa masiku 150, “Mulungu anakumbukira Nowa . . . , ndipo Mulungu anapititsa mphepo pa dziko lapansi, naphwa madzi.” (Genesis 8:1) Zaka mazana angapo pambuyo pake, Samsoni, atachititsidwa khungu komanso kumangidwa ndi Afilisti, anapemphera kuti: “Yehova, Mulungu, mundikumbukire, ndikupemphani, ndi kundilimbitsa, ndikupemphani, nthaŵi ino yokha.” Yehova anam’kumbukira Samsoni mwa kum’patsa mphamvu zoposa zaumunthu kotero kuti athe kubwezera yekha chilango pa adani a Mulungu. (Oweruza 16:28-30) Ponena za Nehemiya, Yehova anadalitsa zoyesayesa zake, ndipo kulambira koona kunabwezeretsedwa m’Yerusalemu.

“Zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo,” analemba motero mtumwi Paulo. (Aroma 15:4) Ngati tikumbukira Yehova mwa kufuna kuchita chifuno chake, monga momwe anachitira atumiki ake okhulupirika m’mbuyomo, tingakhale ndi chikhulupiriro chakuti Yehova adzatikumbukira mwa kutithandiza kupeza zofuna zathu za tsiku ndi tsiku, mwa kutichirikiza m’mayesero athu, ndiponso mwa kutipulumutsa pamene adzadzetsa chiweruzo pa anthu opanda umulungu.​—Mateyu 6:33; 2 Petro 2:9.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena