Linawavekanso Mphete Kuzala Zawo
“TAONANI zala zanga. Kodi mukuona kusiyana kulikonse?” Mwamuna wina anasonyeza dzanja lake kwa mkazi wina wa Mboni za Yehova, amene ataona anazindikira kuti analibenso mphete yaukwati. Mwamunayo anafotokoza kuti iye ndi mkazi wake anasiya kumvana, ndiye anaganiza zosudzulana. “Iyayi!” inatero Mboniyo. “Tengani buku ili mukaŵerenge. Lidzakuthandizani m’banja lanu.” Ndiye anam’patsa buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku moyo Wosatha lozikidwa pa Baibulo.a
Patapita masiku angapo mwamuna uja anabwera kwa Mboni ija ali wosangalala. Anaionetsa Mboni ija dzanja lake. Tsopano anali atavalanso mphete yaukwati ija. Anaiuza kuti iye pamodzi ndi mkazi wake anaŵerenga buku la Chidziwitso, ndipo tsopano akusangalala. Bukuli linawavekanso mphete kuzala zawo.
Uphungu wa Baibulo ungathandize mwamuna ndi mkazi wake kusonyezana chikondi chenicheni. Izi zili choncho chifukwa chakuti wolemba Baibulo si wina ayi, koma Mlengi wathu, amene akuti: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.”—Yesaya 48:17.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.