Chimene Chimam’soŵa Akakumbukira Mzinda wa New York
CHIKWANGWANI chomwe chikuoneka panopa chakhala pamalo oonekera pa imodzi ya nyumba za fakitale ya Watchtower Society ku Brooklyn, New York, chiyambire m’ma 1950. Anthu opita ku ntchito, alendo, komanso ena amene amangodutsa ndi njira amakumbutsidwa kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku. Kalata yotsatirayi, yochokera kwa Mboni yachitsikana, ikusonyeza mphamvu ya chikumbutso chimenechi.
“Ndinkakambirana ndi mzanga wa m’kalasi zimene ndimafuna kudzachita ndikadzamaliza sukulu yasekondale. Ndinayamba kumuuza za Beteli, likulu la Mboni za Yehova, ndipo anachita chidwi kwabasi. Anandiuza kuti wakhala mu mzinda wa New York moyo wake wonse. Banja lake silinali lokonda za chipembedzo kwenikweni, koma m’maŵa uliwonse iye amati akayang’ana kunja pazenera, amaona chikwangwani choti ‘Ŵerengani Mawu a Mulungu Baibulo Loyera Tsiku ndi Tsiku.’ Ndipo tsiku ndi tsiku amaŵerenga Baibulo lake asanapite kusukulu.
“Atasamuka mu mzindawu, ananena kuti chinthu chimene chimam’soŵa akakumbukira mzinda wa New York n’chakuti akadzuka, saonanso chom’kumbutsa kuŵerenga Baibulo lake. Koma chifukwa cha chikwangwani chomwe chili panyumba ya Watchtower, kuŵerenga Baibulo kwakhala chizoloŵezi chake, choncho akupitirizabe kuŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku!”
Ndi njira yabwino kuyamba tsiku mwa kuŵerenga chigawo cha Mawu a Mulungu! Mwa kutero, mosakayikira mudzawamvetsa mawu a mtumwi Paulo akuti: “Malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Kristu Yesu.”—2 Timoteo 3:15-17.