Kupatsa Kumene Kumakondweretsa Yehova
Kalata yotsatirayi inalandiridwa ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Mozambique:
“Ndine mnyamata wazaka zisanu ndi ziŵiri zakubadwa. Ndimapita kusukulu ya pulaimale. Ndikutumiza ndalama iyi yomwe ndinaipeza mwa kuŵeta nkhuku yanga. Ndinagulitsa nkhuku imeneyo pamtengo wa 12,000 Metikashi [1 dola ya U.S.]. Ndikuthokoza Yehova chifukwa chokuza mwanapiye wanga woyamba kuŵetayo kukhala tambala wamkulu. Ndikufuna kuti mphatso yangayi igwiritsidwe ntchito kuchirikiza Ufumu wa Yehova.”
“P.S. Bambo anga anandithandiza kulemba kalata ino.”
Anthu ena akamva za kuolowa manja amangoganizira za anthu okhawo amene ali ndi chuma chambiri. Komabe, pamene tiŵerenga nkhani ya m’Baibulo yokhudza mkazi wamasiye yemwe anaponya “timakobiri tiŵiri” mosungiramo ndalama, tingazindikire kuti kuolowa manja sikupimidwa ndi kuchuluka kwa zoperekazo, koma ndi kufunitsitsa kwanu kupereka ndi mtima wonse.—Luka 21:1-4.
Yehova amayamikira mphatso iliyonse, ngakhale ikhale yochepa chotani, malinga ngati ikuperekedwa kuchokera pansi pa mtima mosonkhezeredwa ndi chikondi. Ndipotu iye amadalitsa omwe amatsanzira kuolowa manja kwake mwa kupereka nthaŵi yawo, nyonga zawo, kapena chuma chawo pochirikiza Ufumu wake.—Mateyu 6:33; Ahebri 6:10.