Chikondi Chachikristu—Si Nkhani Yongolankhula Chabe
PAMENE moto unatentha nyumba ya banja la a Bartholomew ku Trinidad, zinthu zawo zonse zinawonongeka kungotsala miyoyo yawo. Wachibale amene amakhala pafupi nawo anawapatsa malo okhala. Koma nkhaniyo sinathere pomwepo.
Olive Bartholomew ndi wa Mboni za Yehova. Ndipo a mumpingo umene iye amatumikiramo—komanso ena a m’madera ozungulira—anayamba kusonkha zopereka kuti amangenso nyumba ya banja lawo imene inawonongekayo. Komiti inakhazikitsidwa kuti iyang’anire ntchito yomanganso imeneyo, ndipo kumangako kunayambika. Pafupifupi Mboni 20, pamodzi ndi oyandikana nawo, anafika pamalowo. Ngakhale achinyamata anathandiza nawo ntchitoyo, pamene ena anathandiza kugaŵa zoziziritsa kukhosi.
“Akwathu anasoŵa chonena,” anatero Olive, monga mmene inanenera nyuzipepala ya ku Trinidad yotchedwa Sunday Guardian. “Si a Mboni, ndipo mwamuna wanga adakali wozizwabe ndi zimene akuona.”
Pofotokoza mwachidule za khama lawo, woyang’anira ntchito yomangayo ananenetsa kuti ntchito zonga zimenezi ndizodi zizindikiro za Chikristu choona. “Sitimangopita kunyumba ndi nyumba kukalankhula za chikondi,” anatero. “Tikuyesetsa kuchita zimene timalalikira.”—Yohane 13:34, 35.
[Chithunzi patsamba 32]
Olive Bartholomew ndi mwamuna wake