“Chitsanzo cha Mgwirizano”
UMENEWO ndiye unali mutu wa nkhani mu nyuzipepala ya ku Indaiatuba mu mzinda wa São Paulo ku Brazil. Kodi ndani anasonyeza chitsanzocho? Mlembi wa nyuzipepalayo anati, “Mboni za Yehova, zimene zikukonzekera kumanga ‘Nyumba ya Ufumu,’ monga momwe akachisi awo kapena nyumba zawo zosonkhaniramo zimatchedwera, zikusonyeza chitsanzo chabwino komanso chenicheni cha kugwirizana chimene sitingakane.”
Mgwirizano pakati pa Mboni za Yehova umasonyezedwa pa zochitika ngati zimenezi. Nkhaniyo inatinso: “N’zosangalatsa kuona amuna, akazi, ndi achinyamata modzifunira akugwira ntchito pamodzi modzipereka kumanga malo amene azisonkhanapo kuti alambire Mulungu.”
Mboni za Yehova zimasonyeza chitsanzo chabwino m’njira zinanso. Nkhaniyo inawonjezanso kuti: “Kuphatikiza pa kuphunzira ndi kupemphera, cholinga chawo ndi kuthandiza zidakwa ndi oloŵerera m’mankhwala osokoneza bongo ndi kusonyeza anthu mmene angagwirizanire ndi kukondana.” Kodi zimakwanitsa bwanji zimenezi? Mbonizo zimadziŵa kuti kuphunzira ndi kugwiritsa ntchito uphungu wa Baibulo kumathandiza munthu kumasuka ku mikhalidwe yoipa. N’chifukwa chake zimayesetsa kuphunzitsa ena zimene zaphunzira m’Baibulo. Nkhaniyo inamaliza ndi kuti: “mosakayikira, ndi chitsanzo chimene chiyenera kutsatiridwa.”
Aliyense ndi wolandiridwa ku misonkhano ya Mboni za Yehova ndipo sipakhala kusonkhetsa ndalama. Mukupemphedwa kukafika pa Nyumba ya Ufumu ya pafupi nanu.