Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w00 11/1 tsamba 32
  • Kodi Mtendere wa Dziko Lonse Udzakhalapo Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mtendere wa Dziko Lonse Udzakhalapo Motani?
  • Nsanja ya Olonda—2000
Nsanja ya Olonda—2000
w00 11/1 tsamba 32

Kodi Mtendere wa Dziko Lonse Udzakhalapo Motani?

KODI mtendere wa dziko lonse uli pafupi? Anthu ambiri anaganizapo choncho koma akukayikira tsopano. Malinga ndi nkhani yonena za mavuto a tsogolo lathu, imene anaisindikiza m’nyuzipepala yotchedwa Daily Mail & Guardian ya ku South Africa, “zimene anthu ananeneratu zaka 10 zapitazo za mgwirizano watsopano pandale za mayiko zikuoneka kuti n’zosadalirikanso tsopano.”

Olembawo anafotokoza za mzimu wachidaliro umene unafalikira zaka khumi zokha zapitazo. Nkhondo ya Mawu inali itangotha, ndipo kunalibenso kukangana kwa mayiko amphamvu kwambiri. Chifukwa cha zimene zinaoneka kukhala ngati chiyambi cha nyengo yatsopano yapadera, ambiri anaganiza kuti anthu adzayamba kuchita zamphamvu pothetsa umphaŵi, matenda, ndi mavuto a zachilengedwe. “Zoneneratu zimenezo zikuoneka kukhala zosatheka n’komwe tsopano,” inatero nkhaniyo. “Kukangana kwinanso kwabuka m’madera amene sitinali kuwaganizira n’komwe; umphaŵi padziko lonse ukunkirankira patsogolo. Pali mayiko aŵiri atsopano amene ali ndi zida zanyukiliya. Mbiri ya UN yaipa kwambiri chifukwa cholephera kuchitapo kanthu mwamsanga pa mavuto otsatizana a anthu. Mkhalidwewo ukuchoka pabwinopo kufika poipiratu.”

Ophunzira Baibulo amadziŵa kuti kuyesetsa kwa anthu, kaya zolinga zawo zikhale zabwino motani, sadzakwanitsa bwinobwino. Chifukwa? Chifukwa Baibulo limati, “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Potsogoleredwa ndi Satana, dziko lonse silingafike kukhala ngati Paradaiso mmene Mulungu analilengera.

Panthaŵi imodzimodziyo, pali chifukwa choyembekezera zabwino. Yehova Mulungu amalonjeza kuti adzabweretsa mtendere wa dziko lonse, osati mwa kungokonza mbali zowonongeka m’dongosolo lino la zinthu, koma mwa kubweretsa “dziko latsopano” limene “mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) Inde, chifukwa cha Ufumu wa Mulungu, dziko lathu lapansi lidzasintha kukhala lamtendere, mudzi wachimwemwe, mmene moyo ndi ntchito zidzakhala zosangalatsabe kwa anthu onse omvera. Komanso, Mulungu amalonjeza kuti “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa.” Maziko a malonjezo ameneŵa si maulosi osadalirika operekedwa ndi anthu ayi. Koma ali Mawu osalephera a Mlengi wathu, amene sanama.​—Chivumbulutso 21:4; Tito 1:2.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena