Kukongola kwa M’kati Kuli Ndi Phindu Losatha
“MNYAMATA AMAONA NGATI KUKONGOLA NDIKO UBWINO,” ANATERO MKRISTU WACHIKULIRE WOKHULUPIRIKA.
Inde, kwa nthaŵi yaitali anthu akhala ndi chizoloŵezi choyang’ana kwambiri kukongola kwakunja, zimene zimawachititsa kuganiza molakwa za mtima wa munthu. Komabe, Mlengi wathu amayang’ana zimene ifeyo tili m’kati mwenimweni, kaya thupi lathu lioneke motani. Mwakutero amapereka chitsanzo chabwino kwambiri cha kuganiza kwa uchikulire. Malinga ndi mmene Baibulo limanenera, Mulungu iyemwini anati: “Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.”—1 Samueli 16:7.
Mulungu ndiye Gwero la kukongola kwenikweni kwaumunthu, ndipo Mawu ake amasonyeza kuti pofuna kudziŵa ubwino weniweni wa munthu, mikhalidwe yauzimu ndiyo yofunika kwambiri. Baibulo limati: “Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.” (Miyambo 31:30) Ndithudi, kukongola kwa kunja kungaphimbe kuipa kwa m’kati. (Estere 1: 10-12; Miyambo 11:22) Ngakhale kukongola kwa thupi kungafwifwe popita nthaŵi, kukongola kwa m’kati—mikhalidwe ya mtima—ingakule ndi kukhalapobe.
Choncho, ndi bwino kwambiri kuti tikulitse mikhalidwe monga chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, ndi chiletso! (Agalatiya 5:22, 23) Mwa njira imeneyo tingapeze kukongola kwa m’kati, kumenedi kuli ndi phindu losatha.—1 Petro 3:3, 4.