Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w01 2/15 tsamba 32
  • Kuthetsa Umphaŵi—Kodi N’kosatheka?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuthetsa Umphaŵi—Kodi N’kosatheka?
  • Nsanja ya Olonda—2001
Nsanja ya Olonda—2001
w01 2/15 tsamba 32

Kuthetsa Umphaŵi​—Kodi N’kosatheka?

ALENDO okacheza ku United Nations ku New York City amaona nyumba yotchedwa Economic and Social Council Chamber ili ndi mapaipi komanso nthambo zoonekera ku denga m’chipinda chake chochezeramo. Woonetsa alendo malo anafotokoza kuti: “Kudenga ‘kosatsirizaku’ kwenikweni n’chizindikiro chokumbutsa kuti ntchito ya zachuma ndiponso yachikhalidwe cha anthu ya United Nations siitha; nthaŵi zonse padzakhalabe zambiri zoti zichitidwe pofuna kutukula miyoyo ya anthu padziko lonse.

Ngakhale kuti bungweli likuyesetsa kulimbikitsa ntchito yaphindu yoti anthu onse akhale ndi moyo wapamwamba, ntchitoyi ikuoneka kuti siingathe. N’zochititsa chidwi kuti m’nthaŵi ya utumiki wa Yesu Kristu padziko lapansi m’zaka za zana loyamba C.E., iye anati: “Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka uthenga wabwino.” (Luka 4:18) Kodi “uthenga wabwino” umene ankaulengezawo unali wotani? Unalitu uthenga wonena za Ufumu umene Yehova Mulungu, yemwe wakhala ‘linga la aumphaŵi . . . m’kuvutika kwawo’ adzakhazikitse pamodzi ndi Yesu Kristu monga Mfumu. Kodi Ufumuwo udzachita zotani? Yesaya analosera kuti: ‘Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino. Iye adzameza imfa ku nthaŵi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse.’​—Yesaya 25:4-6, 8.

Kodi mungakonde kudziŵa zambiri za mmene Ufumu wa Mulungu ‘udzatukulire miyoyo ya anthu padziko lapansi,’ kotero kuti sipadzakhalanso aumphaŵi? Ngati ndi choncho, onani m’munsimu kuti mudziŵe m’mene mungapezere mphunzitsi wodziŵa bwino kuti akusonyezeni zambiri zomwe Baibulo limanena pankhani ngati zimenezi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena